Kusinkhasinkha Kumene Kumapindulitsa
Lingaliro la Baibulo
Kusinkhasinkha Kumene Kumapindulitsa
“MAWU A M’KAMWA MWANGA NDI MAGANIZO A M’MTIMA WANGA [“KUSINKHASINKHA KWA M’MTIMA MWANGA KUVOMEREZEKE,” NW] AVOMEREZEKE PAMASO PANU, YEHOVA, THANTHWE LANGA, NDI MOMBOLO WANGA.”—SALMO 19:14.
KODI “kusinkhasinkha” kumatanthauzanji kwa inu? Ngati mumakhulupirira ziphunzitso za zipembedzo zina za ku mayiko a Kum’maŵa, mungakhulupirire kuti ndi chinthu chimene chimathandiza kukhala ndi maganizo ozindikira bwino zinthu kapena kudziŵa zinthu mwapadera. Kusinkhasinkha kwa chipembedzo cha Chibuda kumalimbikitsa kuchotsa malingaliro onse m’maganizo. Mitundu ina ya kusinkhasinkha imanenedwa kuti imalimbikitsa kudzaza maganizo ndi “mfundo zenizeni za nzeru zapadziko lonse.”
Lingaliro la Baibulo pa kusinkhasinkha ndi losiyana ndi zimenezi. Motani? Talingalirani chitsanzo cha m’Baibulo cha mwamuna wotchedwa Isake, amene anali ndi zambiri zosinkhasinkha pausinkhu wa zaka 40. Genesis 24:63 amati: “Isake anatuluka kulingalira [“kusinkhasinkha,” NW] m’munda madzulo.” Palibe chifukwa choganizira kuti Isake anachotsa malingaliro onse m’maganizo ake kapena kuti ankangoyerekezera ‘choonadi cha nzeru za padziko lonse.’ Mosakayikira, Isake anali ndi zinthu zapadera zoti asinkhesinkhe, monga tsogolo lake, imfa ya amayi ake, kapena amene akanadzakhala mkazi wake. Anagwiritsa ntchito nthaŵi yake yapadera usiku moyenera kuti asinkhesinkhe zinthu zofunika kwambiri zimenezo. M’Baibulo, kusinkhasinkha si kungolota uli maso.
Kusinkhasinkha Kumatanthauza Zambiri
Talingalirani chitsanzo cha wamasalmo Davide. Mosakayikira anakumana ndi mavuto othetsa nzeru, ndipo anadziŵa bwino lomwe kuti pokhala munthu wopanda Salmo 19:14, Davide anati: “Mawu a m’kamwa mwanga ndi maganizo [“kusinkhasinkha kwa m’mtima wanga kuvomerezeke,” NW] amumtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.” Mawu achihebri opezeka pano otembenuzidwa kuti “kusinkhasinkha” amatanthauza “kudzilankhulira wekha.” Inde, Davide “anadzilankhulira yekha” zokhudza Yehova, zochita zake, malamulo ake, ndi chilungamo chake.—Salmo 143:5.
ungwiro, anafunikira thandizo la Mulungu kuti akhale ndi khalidwe labwino. Kodi chinam’limbikitsa Davide n’chiyani kuti apirire mikhalidwe yovuta? Monga momwe kwalembedwera paMofananamo, Akristu oyambirira anaona kupatula nthaŵi yosinkhasinkha zinthu zauzimu kukhala mbali yofunika ya kulambira koona. Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” (Afilipi 4:8) Inde, kuti tikhale ndi malingaliro omangirira, “zinthu” zimenezi zimene Paulo anatchula zifunikira kuloŵa m’maganizo athu nthaŵi ina. Motani?
Wamasalmo akupereka yankho. Pa Salmo 1:1, 2 timaŵerenga kuti: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa . . . M’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” Inde, wamasalmo ankaŵerenga chilamulo cha Mulungu nthaŵi zonse. Ndiyetu ankatha kusinkhasinkha pa zinthu zimene amaphunzira zokhudza Mlengi.
Kusinkhasinkha Lerolino
Kuŵerenga Baibulo n’kwaphindu, koma tikaŵerenga, tiyenera kusinkhasinkha, kuganiza mozama, kapena “kudzilankhulira tokha” pa zimene taŵerengazo. Monga momwe kugaya chakudya kulili kofunika ngati titi tipindule mokwanira ndi chakudya chomwe timadya, kusinkhasinkhanso n’kofunika ngati tikufuna kumvetsa zimene timaŵerenga m’Baibulo. Kusinkhasinkha koyenera kumachita zazikulu kuposa kungochotsa malingaliro olakwika. Kumatipatsanso mpata wopezera mayankho ochokera m’Baibulo othetsera mavuto athu. Kusinkhasinkha kotero kungatithandize kuthetsa zodandaulitsa za moyo wa tsiku ndi tsiku.—Mateyu 6:25-32.
Wamasalmo Davide anazindikira kufunika kwa kusinkhasinkha pokondweretsa Mulungu. Anati: “Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru.” (Salmo 37:30) Inde, kusinkhasinkha ndicho chizindikiro cha wolambira wokhulupirika. Kuti tiŵerengedwe olungama ndi Mulungu ndi dalitso lalikulu, ndipo zimabweretsa mapindu auzimu. Mwachitsanzo, Baibulo limati “mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa m’banda kucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.” (Miyambo 4:18) N’chifukwa chaketu Mkristu womvera yemwe ‘amalankhula mwanzeru’ angayembekezere kukula m’kumvetsetsa kwake Baibulo.
Baibulo limalangizanso Akristu kuti asinkhesinkhe pa maudindo awo a m’Malemba. Mtumwi Paulo anauza Timoteo kuti: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse. Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:15, 16) Inde, zimene timanena ndi zimene timachita zingakhudze kwambiri ena.
Mwachionekere, tili ndi zifukwa zambiri zotipangitsa kulingalira ndi kuganiza mozama pa zinthu zofunika. N’kwanzerutu kuti tikumbukire zomwe zinatichitikira kale, kuganiza zinthu zapanopo, ndiponso kuti tilingalire moyenera za m’tsogolo mwathu. Koma koposa zonse, kusinkhasinkha kwathu kudzatipatsa chidziŵitso chapamwamba ngati tiika maganizo athu pa nzeru za Mlengi wathu, Yehova Mulungu.
[Chithunzi patsamba 29]
“Woganiza” chopangidwa ndi Rodin