Kuchoka ku Olympia Kukachitira ku Sydney
Kuchoka ku Olympia Kukachitira ku Sydney
ANTHU ambiri amaona kuti Maseŵera a Olimpiki ndiwo mpikisano wolimbitsa thupi wofunika koposa padziko lonse. “Palibe maseŵera ena amene amakopa chidwi cha anthu ambiri ngati ameneŵa,” imatero The World Book Encyclopedia. “Anthu mamiliyoni angapo amapita kukaonera maseŵeraŵa, ndipo ena miyandamiyanda padziko lonse amawaonera pa wailesi yakanema.”
Mbiri Yake Mwachidule
Maseŵera a Olimpiki anayamba kalekale zaka zikwizikwi zapitazo. Pokhulupirira kuti ochita maseŵeraŵa amakondweretsa mizimu ya anthu akufa, Agiriki akale anali kuchita mapwando a dziko lawo lonse omwe ankaphatikiza kupembedza ndi maseŵera. Ena mwa mapwandoŵa anali maseŵera otchedwa Isthmian, Nemean, Olimpiki, ndiponso Pythian. Pamaseŵera onseŵa, maseŵera a Olimpiki ndiwo anali olemekezeka zedi chifukwa chakuti anali kuchitira ulemu Zeu, amene Agiriki ankam’khulupirira kuti ndiye mfumu ya milungu yonse.
Mwachionekere pamaseŵera a Olimpiki oyambirira pankangochitika mpikisano wothamanga wokha basi. Koma m’kupita kwanthaŵi anawonjezera mipikisano ina monga kuyendetsa galeta ndiponso maseŵera olimba kwabasi oyesana kupirira. Alendo anali kubwera mwaunyinji kuchokera ku mbali zonse za dziko kudzaonera maseŵeraŵa. Pofuna kuonetsetsa kuti alendoŵa ali otetezedwa, anakhazikitsa pangano loletsa nkhondo panthaŵi ya maseŵeraŵa ndiponso pambuyo pake.
Pamene Roma anayamba kulamulira, maseŵera a Olimpiki anayamba kutha. Inde, Aroma ambiri anali kudana ndi maseŵera osiyanasiyana. Mfumu Nero yekha ndiye ankakonda maseŵera. Iye anachita nawo maseŵeraŵa m’chaka cha 67 C.E. ndipo anapambana m’mbali iliyonse imene iye anaseŵera nawo. Zikuoneka kuti amene ankapikisana naye anali kudziŵa kuti zinthu siziwayendera bwino akam’posa! Mulimonse mmene zinaliri, pomwe chimafika chaka cha 394 C.E., maseŵera a Olimpiki anali atalekeka.
Kuyambikanso kwa Maseŵera a Olimpiki
Patapita zaka 1,500, zinthu zimene anthu ofukula m’mabwinja a ku Germany anapeza pa chigwa cha mzinda wa Olympia wakale zinadzutsa chidwi chatsopano m’maseŵeraŵa. Kenako, Mfalansa wina wazaka 29 zakubadwa wotchedwa Baron Pierre de Coubertin, anapereka lingaliro lakuti maseŵeraŵa ayambikenso. Chotero, mu 1896 Maseŵera a Olimpiki oyamba ochitidwa mwamakono anachitika ku Athens. Kuyambira chaka chimenecho, maseŵera a Olimpiki akhala akuchitika m’zaka zisanu zilizonse mosalephereka wamba.
Lerolino anthu ambiri amayembekezera mwachidwi maseŵeraŵa. Chaka chino, maseŵeraŵa adzachitikira ku Sydney, Australia, kuyambira pa September 15 mpaka pa October 1. Kumeneko kudzakhala maseŵera osiyanasiyana 28, magulu azochitika okwana 292, komanso zigawo zokwana 635, ndipo oseŵera osiyanasiyana 10,300 adzachita nawo mpikisanowo.
Komabe, m’zaka zaposachedwapa, maseŵera a Olimpiki ayambitsa mikangano. Anthu ena ambiri afika ponena kuti zolinga za Olimpiki zakanika. Mukaona zomwe zimachitika kuseri kwake mudabwa kudziŵa kuti zinali zobisika kwa inu ndiponso mulephera kumvetsa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 19]
Scala/Art Resource, NY