Nkhani za pa TV—Kodi Ndi Zambiri Motani Zimene Zimakhala Zofunikadi?
Nkhani za pa TV—Kodi Ndi Zambiri Motani Zimene Zimakhala Zofunikadi?
Pambuyo pofufuza nkhani zokwanira 102 zoulutsidwa pa TV m’mizinda 52 ya United States pofuna kuona zimene zimakhala m’nkhani ndiponso kaulutsidwe ka nkhanizo, bungwe lina loona zofalitsa nkhani linapeza kuti 41.3 peresenti yokha ya mapulogalamu oulutsa nkhani ndi yomwe inalidi ndi nkhani. Kodi mbali ina ya nkhanizo imakhala chiyani?
Pa avareji, 30.4 peresenti ya nthaŵi imene ma TV a m’dzikomo amaulutsira nkhani imakhala ya nthaŵi yotsatsira malonda. Ndithudi, ena mwa mawailesi akanema amene anafufuzidwa anali kuthera nthaŵi yochuluka pa kutsatsa malonda kusiyana ndi nkhani. Kuwonjezera pamenepo, nthaŵi youlutsira nkhani kaŵirikaŵiri imakhala yodzaza ndi nkhani zosathandiza, linatero lipotilo pofotokoza mwachidule zimene kafukufukuyo anapeza. * Pamutu wakuti “Nkhani Zosathandiza,” lipotilo linatchulapo “nthaŵi yochuluka youlutsira nkhani yomwe imathera pa macheza pakati pa anthu oulutsa nkhani, kutchukitsa chinthu chinachake ndi kuonetsa nkhani zomwe ziulutsidwe m’tsogolo, nkhani za ‘zolingalira za munthu ndiponso za mmene iye akumvera’ kapena nkhani zopanda pake ndi nkhani zokhudza anthu otchuka.” Zina mwa nkhani zosathandiza ndi monga izi: “Mpikisano wa Mawu Oipa Kwambiri a Amuna Achikulire,” “Mtolankhani Ayenda Ulendo ‘Woopsa, Wovuta Kuukhulupirira, Wodabwitsa’ pa Sitima ya ku Malo Amaseŵera,” ndi “Anthu Ambiri Akugula Zakudya Zopangira Masangweji m’Sitolo Zikuluzikulu.”
Kodi ndi nkhani zotani zimene zimapanga nkhani zenizenizo? Nkhani za chiwawa zimatenga mbali yaikulu ya nkhani za pa TV, yokwanira 26.9 peresenti ya nthaŵi youlutsira nkhani. “Mawu akuti ‘Ngati ndi nkhani yonena za chiwawa kapena kuvulazana, imakhala nkhani yotsogola kwambiri’ n’ngoona ponena za nkhani za pa ma TV a m’dzikomo . . . Chiwawa chingakhale chitachepako m’dziko la United States m’kati mwa zaka zoŵerengeka zapitazi, koma sizinatero m’nkhani za pawailesi ya kanema.” Chifukwa chiyani? Malinga ndi olemba lipotili, “nkhani za chiwawa zimakhala zochititsa chidwi kwambiri ndipo anthu ambiri amachita nazo chidwi.”
Zotsatira pambuyo pa nkhani za chiwawa ndi nkhani za masoka monga moto, kugundana kwa magalimoto, kusefukira kwa madzi, ndiponso kuphulika kwa mabomba (12.2 peresenti ya nkhani), motsatidwa ndi nkhani zamaseŵero (11.4 peresenti). Kenako pali nkhani zokhudza zaumoyo (10.1 peresenti), boma (8.7 peresenti), ndi nkhani zachuma (8.5 peresenti). Nkhani monga ngati za maphunziro, chilengedwe, maluso, ndi za sayansi sizilabadiridwa kwenikweni (kuyambira pa 1.3 mpaka 3.6 peresenti). Komanso, lipoti la zanyengo limatenga 10 peresenti ya nkhani zonse. “Aliyense amakonda kunena za nyengo ndipo nkhani za pa TV n’zotero nazonso,” anathirira ndemanga motero ofufuzawo. Anawonjezera ndi kuti: “Mtundu uliwonse wa nyengo, yabwino kapena yoipa, yotentha kapena yozizira, yachinyontho kapena youma, ingapangitse nkhani za pa TV kutenga nthaŵi yaitali zikuulutsidwa.”
Motsimikizira, lipotilo linanena kuti chiŵerengero chomakulakulabe cha atolankhani ndiponso oonerera ma TV chikuona kufunika kwa kusintha. Komabe, kufufuzaku kwasonyeza kuti kusinthako kudzakhala kovuta chifukwa chakuti “kayendedwe ka ntchito za malonda ndiponso umbombo zingamawopsezebe kagwiridwe kabwino ka ntchito ya utolankhani.”
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Lipoti lakuti Not in the Public Interest—Local TV News in America (Zosapindulitsa Anthu—Nkhani za pa ma TV a mu America) ndi lachinayi pa kufufuza kwa pachaka kwa m’dziko lonselo kwa zinthu zimene zimakhala m’nkhani. Lipotili linalembedwa ndi Dr. Paul Klite, Dr. Robert A. Bardwell, ndi Jason Salzman, a Rocky Mountain Media Watch.