Njira Yogonjetsera Kutaya Mtima
Lingaliro la Baibulo
Njira Yogonjetsera Kutaya Mtima
KUTAYA mtima n’kofala pakati pa anthu onse, pamlingo winawake. Komabe, anthu ena amataya chiyembekezo chonse kwakuti imfa imaoneka ngati yabwino poyerekeza ndi moyo.
Baibulo limasonyeza kuti ngakhale atumiki okhulupirika a Mulungu amakhudzidwa ndi mavuto komanso kupanikizika zimene zingawatayitse chiyembekezo. Mwachitsanzo, talingalirani za Eliya ndi Yobu—onse aŵiriŵa anali paubwenzi wabwino kwambiri ndi Mulungu. Atathaŵitsa moyo wake kwa Mfumukazi yoipayo Yezebeli, Eliya ‘anapempha [Yehova] kuti afe.’ (1 Mafumu 19:1-4) Yobu, munthu wolungamayo, anakumana ndi masoka otsatizana, kuphatikizapo nthenda yoipa komanso imfa ya ana ake khumi. (Yobu 1:13-19; 2:7, 8) Kutaya mtima kwake kunam’pangitsa kunena kuti: “Ndikanakonda imfa poyerekeza ndi mavuto anga onse.” (Yobu 7:15, The New English Bible) Mwachionekere, nkhaŵa inaŵakulira kwambiri amuna okhulupirika a Mulungu ameneŵa.
Kwa anthu ena lerolino, kutaya mtima kungayambe chifukwa cha zotsatira zopweteka kwambiri za ukalamba, imfa ya mnzawo wa muukwati, kapena chifukwa cha mavuto aakulu kwambiri a zachuma. Ena amaona kuti kupsinjika maganizo kaŵirikaŵiri, zotsatira za zinthu zosokoneza maganizo, kapena mavuto a banja zimawapangitsa kukhala ngati anthu ovutika pakatikati pa nyanja, funde lililonse likupangitsa kukhala kowavuta kwambiri kuti afike kumtunda. Mwamuna wina anati: “Umadziona ngati munthu wopanda ntchito—ngati kuti palibe adzakusoŵe ukamwalira. Nthaŵi zina sungapirire kukhala wekhawekha.”
M’zochitika zina mikhalidwe imasintha n’kukhala bwino, n’kuthetsa kupsinjika maganizo kumeneku. Koma bwanji ngati mikhalidwe yathu sikusintha? Kodi Baibulo lingatithandize motani kuti tigonjetse kutaya mtima?
Baibulo Lingathandize
Yehova anali wokhoza ndiponso wamphamvu kuchirikiza Eliya ndi Yobu m’zovuta zawo. (1 Mafumu 19:10-12; Yobu 42:1-6) Kudziŵa zimenezo lerolino n’kotitsitsimulatu kwambiri! Baibulo limati: “Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.” (Salmo 46:1; 55:22) Ngakhale zitaoneka kuti kutaya mtima kukutifooketsa, Yehova akulonjeza kuti adzatichirikiza kwambiri ndi dzanja lake lamanja la chilungamo. (Yesaya 41:10) Kodi tingapeze motani chithandizo chimenechi?
Baibulo limafotokoza kuti mwa pemphero “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima [yathu] ndi maganizo [athu] mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Chifukwa cha kutaya mtima, sitingapeze njira yothetsera vuto lomwe tili nalo. Komabe, ngati ‘tilimbika chilimbikire m’kupemphera,’ Yehova angatchinjirize mitima yathu ndi malingaliro athu, n’kutipatsa mphamvu zomwe tifunikira kuti tipilire.—Aroma 12:12; Yesaya 40:28-31; 2 Akorinto 1:3, 4; Afilipi 4:13.
Tidzapindula mwa kukhala olunjika m’mapemphero athu. Ngakhale kuti kungakhale kovuta kufotokoza malingaliro athu, tiyenera kukhala omasuka kuyankhula ndi Yehova ponena za zimene tikuganiza kapena zimene tikuona kuti ndilo gwero la vuto lathulo. Tiyenera kum’pempha mphamvu kuti zitichirikize tsiku lililonse. Tikutsimikizidwa kuti: “[Yehova] adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwawo, nadzawapulumutsa.”—Salmo 145:19.
Kuwonjezera pa kupemphera, tiyenera kupeŵa kukhala patokha. (Miyambo 18:1) Ena alimbikitsidwa chifukwa cha kuthera mphamvu zawo ndiponso nthaŵi yawo pa kuthandiza anthu ena. (Miyambo 19:17; Luka 6:38) Talingalirani za mkazi wina wotchedwa Maria, * amene sanangolimbana ndi matenda a kansa okha komanso anthu asanu ndi atatu a m’banja lake anamwalira m’chaka chimodzi chokha. Maria anadzikakamiza kudzuka pabedi ndi kukapitiriza kugwira ntchito za masiku onse. Pafupifupi tsiku lililonse ankapita kukaphunzitsa ena za Baibulo, ndipo ankafika mokhazikika pa misonkhano yachikristu. Akabwerera kunyumba, Maria amavutikanso kwambiri ndi malingaliro a kutaya mtima. Komabe, mwa kulingalira za momwe iye angathandizire anthu ena, Maria akutha kupirira.
Koma bwanji ngati tikuona kuti n’kovuta kupemphera kapena tikuona ngati kuti sitingathe mwa zoyesayesa zathu kuthetsa mkhalidwe wokhala patokha? Pa mkhalidwe ngati umenewo tiyenera kuyesetsa kuti tipeze chithandizo. Baibulo limatilimbikitsa kutembenukira kwa “akulu a Mpingo.” (Yakobo 5:13-16) Mwamuna wina amene akulimbana ndi kupsinjika maganizo kosatha ananena kuti: “Nthaŵi zina kuyankhula ndi munthu amene umam’dalira kumathandiza kuziziritsa maganizo ndiponso mkhalidwewo, kotero kuti umakhala ndi malingaliro abwino.” (Miyambo 17:17) N’zoona kuti, pamene mukhala ndi nkhaŵa yaikulu kwambiri komanso kwanthaŵi yaitali, zimenezo zimasonyeza kuti pali vuto lofunika mankhwala, ndipo chithandizo choyenera cha akatswiri chingafunikenso. *—Mateyu 9:12.
Ngakhale kuti palibe njira zophweka zothetsera kutaya mtima, sitiyenera kunyozera kuti Mulungu angatithandize kugonjetsa mavuto. (2 Akorinto 4:8) Kulimbikira kupemphera, kupeŵa kukhala patokha, ndiponso kupeza chithandizo choyenera zidzatithandiza kupezanso mphamvu. Baibulo limalonjeza kuti Mulungu adzathetseratu gwero lenileni la kutaya mtima. Akristu amadalira kwambiri pa iye ndi kuyembekezera tsiku pamene “zinthu zakale sizidzakumbukika.”—Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Si dzina lake lenileni.
^ ndime 12 Galamukani! sisankha mtundu uliwonse wa chithandizo. Akristu ayenera kuonetsetsa kuti chithandizo chilichonse chimene akulandira sichikutsutsana ndi mfundo za chikhalidwe za Baibulo. Kuti mudziŵe zambiri onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1988, masamba 25-9.