Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Loida Ayamba Kulankhula

Loida Ayamba Kulankhula

Loida Ayamba Kulankhula

Yosimbidwa ndi mayi ake a Loida

MONGA mayi aliyense wapakati, ndinkadera nkhaŵa kuti mwina mwana wanga adzabadwa ndi vuto linalake. Komabe, sindinayembekezere kuti mwana wanga wachitatu, Loida, adzalira momvetsa chisoni pobadwa. Mwangozi, dokotala anathyola phewa la Loida ndi zida zogwiritsira ntchito pochiritsa amayi apakati. Patapita milungu ingapo chichitireni opaleshoni yom’konza vutoli, Loida anatulutsidwa m’chipatala. Komabe, kusangalala kwathu kunali kwanthaŵi yochepa.

M’miyezi ingapo yotsatira, kunapezeka kuti Loida anali ndi vuto lalikulu. Iye sanali kugwirizana ndi mankhwala amene analandira. Mankhwala ameneŵa, ankaoneka ngati kuti akungobweretsa matenda enanso monga kutentha thupi, kutsegula m’mimba, ndi khunyu ndipo mankhwala a matenda ameneŵa anali kukulitsa vuto lakelo. Mosakhalitsa, ziwalo za thupi la Loida zinayamba kusagwira ntchito molongosoka. Mapeto ake, madokotala anatiuza kuti Loida anali ndi matenda aubongo amene amakhudza ziwalo za thupi otchedwa Cerebral Palsy. Anatiuza kuti sadzayenda kapena kulankhula ngakhalenso kumva zolankhula zathu.

Kuyamba Kuyesa Kuyankhula Naye

Ngakhale kuti madokotala ananena zawo, ndinkaonabe ngati kuti Loida ankatha kumva zinthu zambiri. Chotero ndinali kumuŵerengera mabuku ophweka ndipo ndinayesetsa kum’phunzitsa zilembo. Koma Loida sanali kulankhula, kapenanso kusonyeza kuti anali kumva zimene ndinali kunenazo. Panalibiretu njira yodziŵira kuti anali kumva ngati anali kumva n’komwe.

Pamene zaka zinali kupita, kuyesa kwanga kuphunzitsa Loida kunkaoneka kuti sikunkaphula kanthu. Komabe, ndinkatha maola ambiri ndikumuŵerengera mabuku. Tinamuikanso paphunziro lathu la Baibulo labanja pamodzi ndi Noemí, mwana wanga wamkazi wamng’ono mwa onse, tinali kugwiritsa ntchito buku la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wam’kuruyo ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. * Ndinkamuŵerengera Loida mitu yambiri ya m’mabuku ameneŵa mobwerezabwereza.

Kusamvana ndi munthu amene umam’konda n’kopwetekadi. Ndikapita kupaki ndi Loida, ankalira mosatonthozeka. Chifukwa chiyani? Ndinkaganiza kuti anali kuwawidwa mtima chifukwa sankatha kuthamanga ndiponso kuseŵera monga anali kuchitira ana ena. Nthaŵi ina yake, Loida analira pamene mkulu wake anandiŵerengera nkhani ina ya m’buku la kusukulu. Ndithudi, chinachake chinali kum’soŵetsa mtendere, koma sindinkadziŵa kuti chinali chiyani. Zolankhula za Loida zinali zochepa chabe komanso zosamveka, zinali zongosonyeza zinthu zofunika kwambiri monga chakudya, madzi, kugona, kapena kupita kuchimbudzi.

Ali ndi zaka 9, Loida anayamba sukulu ya ana ofunika chisamaliro chapadera. Komabe, m’zaka zitatu zotsatira, vuto lake linakula kwambiri. Ankaopa kuyenda yekha ngakhale mapazi angapo, ndiponso anasiyiratu kulankhula. Ine ndi mwamuna wanga tinaganiza kuti n’koyenera kum’phunzitsa Loida panyumba.

M’zaka zisanu ndi chimodzi zotsatira, ndinayesetsa kum’phunzitsa Loida zomwe ndikanatha. Ndinkalemba zilembo pa bolodi, ndikumaganiza kuti Loida akopera zilembozo. Koma zoyesayesa zangazo sizinaphule kanthu. Kodi vuto linali kusamva, kapena kuti Loida sakanatha kulemba popeza manja ake sanali kugwira ntchito molongosoka?

Ali ndi zaka 18, Loida anayamba kuvutitsa kwambiri kwakuti ndinapempha Yehova ndi mtima wonse, kuti andithandize kulankhulana ndi mwana wanga. Pemphero langa linayankhidwa modabwitsa.

Ayamba Kulankhula

Nthaŵi imene zinthu zinasintha inali imene ana anga akazi anali kukongoletsa chipinda chathu chogona. Asanakakatule pepala lakale limene linali pakhoma, Noemí analembapo mayina—ena a Baibulo, a anzake ndi a anthu a m’banjamo. Mongofuna kudziŵa, mwana wanga Rut anam’funsa Loida ngati angadziŵe pamene panalembedwa kuti “Yehova.” Mosayembekezera, Loida anapita pakhomalo ndi kuika mutu wake pafupi ndi pamene panalembedwa dzina la Mulungu. Rut ankakayikira ngati Loida angadziŵenso mayina enawo, choncho anam’funsanso. Rut anadabwa kuti Loida anali kuwadziŵa mayina onsewo—ngakhale mayina amene anali asanaonepo atalembedwa! Rut anaitana banja lonse kuti lidzaone lokha. Loida amatha kuŵerenga!

M’kupita kwa nthaŵi, tinapeza njira yom’thandizira Loida “kulankhula” nafe. Tinaika zilembo pakhoma la m’njira yathu yaitali yopita m’zipinda. Kuika zilembozo pa bolodi lonyamula m’manja sibwenzi kuli kothandiza, popeza manja a Loida sanali kugwira ntchito molongosoka kwakuti n’kuloza chilembo chilichonse. Choncho Loida akafuna kulankhula, anali kunena mawuwo mwakupita pa chilembo chimene akufuna pakhomalo. Mukhoza kuona kuti zimenezi n’zotopetsa kwambiri. Ndiponso, Loida anafunika kuyenda ulendo wautali kuti alembe mawu apatsamba limodzi lokha, ndipo zimam’tengera nthaŵi kuti amalize!

Komabe, Loida ndi wokondwa kuti akutha “kulankhula” nafe. Ndiponso, awa ndiwo anali mawu ake oyamba kutiuza: “Ndili wosangalala kwambiri kuti, ndi thandizo la Yehova, tsopano ndikutha kulankhula.” Tinadabwa, ndipo tinam’funsa Loida kuti: “Kodi unali kuchitanji ukakhala tsiku lonse?” Loida anati anali kuganizira zimene anali kulakalaka kuti atiuze. Ndithudi, Loida akuti kwa zaka 18 wakhala akufunisitsa kuti alankhule. “Pamene Rut anayamba sukulu,” iye akutero, “Ndinkaŵerenga ndekha mabuku akusukulu. Ndinkatsegula pakamwa panga n’kumang’ung’udza, koma simunali kumva. N’chifukwa chake nthaŵi zambiri ndinkayamba kulira.”

Ndinapepesa ndikulira posamumvetsetsa. Loida anayankha kuti: “Ndinu mayi wabwino, ndipo simunatope. Nthaŵi zonse ndimasangalala kukhala nanu pamodzi. Ndimakukondani kwambiri. Tontholani. Mwamva?”

Kupita Patsogolo Mwauzimu

Loida anali nacho kale chidziŵitso cha Baibulo, ndipo analoŵeza pamtima mavesi ena a Baibulo. Komabe mosakhalitsa anatiuza kuti anali kufuna kupereka ndemanga pa Phunziro la Nsanja ya Olonda la mpingo, kukambirana Baibulo mwa mafunso ndi mayankho kwamlungu uliwonse. Akanachita bwanji zimenezi? M’modzi wa ife anali kumuŵerengera nkhani yonse. Kenako Loida ankasankha funso limene akufuna kuyankha. Tinkalemba yankho lakelo iye akuloza zilembo. Kenako, pamsonkhano, mmodzi wa ife amaŵerenga yankho la Loidalo. Nthaŵi ina Loida anatiuza kuti: “N’zosangalatsa kuti ndikuchita nawo. Zimenezi zimandipangitsa kudzimva kuti ndine wamumpingomo.”

Pamene anali ndi zaka 20, Loida anafotokoza kuti akufuna kubatizidwa. Atafunsa ngati amadziŵa zimene zimatanthauza kudzipatulira kwa Yehova, Loida anayankha kuti anachita kale zimenezo zaka 7 zapitazo—ali ndi zaka 13 zokha. “Ndinapemphera kwa Yehova,” iye anatero, “ndipo ndinamuuza kuti ndikufuna kum’tumikira kosatha.” Pa August 2, 1997, Loida anasonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi. Loida anatiuza kuti, “ndi thandizo la Yehova, ndachita zimene ndimafunitsitsa!”

Loida amasangalala kukambirana za Ufumu wa Mulungu ndi achibale komanso anansi. Nthaŵi zina amatsagana nafe kukalalikira mu msewu. Analembanso kalata imene timaisiya pakhomo pamene sitinapezepo anthu. Loida amakonda kwambiri okalamba ndiponso odwala. Mwachitsanzo, tili ndi mlongo wina mu mpingo wathu amene anadulidwa mwendo. “Ndikudziŵa mmene zinthu zimakhalira ngati sutha kuyenda,” Loida anatiuza choncho, chotero analemba kalata yom’limbikitsa mlongo ameneyu. Komanso pali kamnyamata kena kotchedwa Jairo, kamene kali mu mpingo winawake, ikoko kanafa ziwalo zonse. Pamene Loida anamva za vuto lakelo, anam’lembera kalata. Mbali ya kalatayo inali yakuti: “Posachedwapa Yehova adzatichiritsa. Mu Paradaiso simudzakhalanso kuvutika. Nthaŵi imeneyo ndidzapikisana nawe kuthamanga. Ndikuseka chifukwa zidzakhala zosangalatsa kwambiri. Kuganiza kuti tidzakhala mmene Yehova anatilengera, wopanda matenda . . . Si zosangalatsa zimenezi?”

Anathandizidwa Kupirira

Tsopano ndikuzindikira bwino chifukwa chimene Loida ankachitira zinthu zinazake zimene zinkandidabwitsa. Mwachitsanzo, Loida akuti ali mwana sankafuna kumukumbatira chifukwa anali wokhumudwa kwambiri. “Zinkaoneka ngati kukondera zedi kuti achemwali anga azilankhula ndi kuphunzira zinthu koma ineyo ayi,” iye akutero. “Zinkandinyansa kwambiri. Nthaŵi zina ndinkangofuna n’tafa.”

Ngakhale akulankhula, Loida akukumana ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, pafupifupi mwezi uliwonse amakomoka kangapo ndipo amachita ngati watsamwa komanso mikono ndi miyendo yake imapulukutapulukuta. Kuphatikiza apo, matenda alionse, ngakhale chifuwa chenichenichi amafooka nacho kwambiri. Nthaŵi zina Loida amavutika maganizo chifukwa cha matenda akewo. N’chiyani chimene chimam’thandiza kupirira? M’lekeni akuuzeni yekha:

“Pemphero lakhala lothandiza kwambiri. Ndimasangalala kwambiri polankhula ndi Yehova, ndi kukhala naye pafupi. Ndikuyamikiranso chikondi komanso chisamaliro cha ena pa Nyumba ya Ufumu. Ndimaona kuti ndili ndi mwayi waukulu kuti ngakhale ndili ndi matendawa, ndaleledwa ndi makolo aŵiri abwino kwambiri amene amandikonda zedi. Sindidzaiŵala zimene achemwali anga andichitira. Malembo okongola amene anawaika pakhoma paja anapulumutsa moyo wanga. Pachipanda chikondi cha Yehova ndi cha banja langa, bwenzi moyo wanga uli wopanda tanthauzo.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. Buku la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wam’kuruyo analeka kulisindikiza.

[Chithunzi patsamba 24]

Loida ndi a m’banja lake