Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Linandithandiza Kupenda Moyo Wanga’

‘Linandithandiza Kupenda Moyo Wanga’

‘Linandithandiza Kupenda Moyo Wanga’

ZIMENEZO n’zimene Maria mtsikana wa zaka 18 wochokera mumzinda wa Cherepovets ananena zokhudza buku lotchedwa Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Iye analembera mawu otsatiraŵa ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova imene ili pafupi ndi St. Petersburg, ku Russia, mtunda wa makilomita 400 kuchokera ku Cherepovets.

“Buku limeneli landithandiza kudzipenda, kupenda zolinga zanga ndiponso kupenda anthu amene ndimakhala nawo. Ndinapeza mayankho a mafunso amene akundikhudza kwambiri kuposa onse. Pamene ndinali kuŵerenga bukuli, sindinathe kudziŵa kuti ndingathokoze bwanji moti ndinatuluka misozi posoŵa chochita.”

Maria anawonjezera kuti: “Zinkakhala ngati kuti maso anga anaphimbidwa ndi chinsalu ndipo tsopano achimasula, ndipo anali atatsegukiratu pofuna kuonetsetsa. Buku limeneli n’labwino koposa mabuku onse amene ndaŵerengapo m’moyo wanga. Popeza kuti n’lozikidwa m’Baibulo ndiponso kuti malangizo a Yehova ndi abwino koposa, palibiretu lofanana nalo.”

Ngati inunso mukufuna kupindula ndi chidziŵitso cha m’buku lotchedwa Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, mungalandire buku lanu mwa kulemba zofunika pa silipi lotsatirali ndi kutumiza ku adiresi yosonyezedwa pamenepo kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa pa tsamba 5 la magazini ano.

□ Nditumizireni buku lotchedwa Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.