‘Iwo Anali Osangalatsa!’
‘Iwo Anali Osangalatsa!’
POSACHEDWAPA, manijala wamkulu wa hotela ina pafupi ndi bwalo lina la ndege lalikulu kwambiri ku Japan anakacheza ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Ebina. Ankaoneka kuti anali wokondwa kwambiri. Kodi n’chifukwa chiyani anatero?
M’kati mwa 1998, Mboni zoposa 200 zinakhala pa hotela ya manijalayo pa nthaŵi yomwe zinkapita ndi kubwerera ku misonkhano yawo yamayiko ku Africa, Australia, Korea ndi North America. Pamene wogwira ntchito pa hotelayo anakumana kuti aonenso momwe ntchito yayendera m’chaka chapitacho, iwo ananena kuti mwa alendo 30,000 amene hotelayo imalandira pachaka, alendo amene anali kupita ku msonkhano aja anali ochititsa chidwi koposa onse.
Choncho, manijala wa hotelayo anapita ku Ebina kukathokoza. Iye anati, ‘Alendo amene aja, anali aulemu zedi ndiponso anasiya zipinda zawo zili zaukhondo ndi zoyera. Kaŵirikaŵiri anali kuthokoza. Kuphatikiza apo, anali kupereka mawu olimbikitsa kuchokera m’Baibulo. Analidi osangalatsa zedi!’
Manijalayo anapitiriza kuti: ‘Timalandira alendo ambiri ovutika. Chotero takhala tikufunafuna chidziŵitso chothandizira anthu otereŵa. Tikufuna kuti iwo apindule ndi ziphunzitso za Baibulo chifukwa zimasonkhezera bwino miyoyo ya anthu.’
N’chifukwa chake, manijalayo anafunsira makope 80 a zofalitsa za Mboni za Yehova zosiyanasiyana kuti akaziike m’chipinda cha hotelayo. Mwa zofalitsa zomwe anafunsira panali buku la masamba 192 lotchedwa Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Ngati mukufuna kope lanu, chonde lembani zofunika pa silipi lotsatirali ndipo tumizani ku adiresi yosonyezedwa pamenepo kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5 la magazini ano.
□ Nditumizireni buku lotchedwa Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.