Onani Uthenga wa M’Baibulo Mwachidule
Yehova analenga Adamu ndi Hava kuti akhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Satana anaipitsa dzina la Mulungu ndipo anasonyeza kuti Mulungu siwoyenera kulamulira. Adamu ndi Hava anagwirizana ndi Satana pogalukira Mulungu ndipo zimenezi zinachititsa kuti iwowo ndiponso ana amene anabereka akhale ochimwa ndiponso ayambe kufa
Yehova anaweruza ochimwawo ndipo analonjeza kuti kudzabwera Mpulumutsi, kapena kuti Mbewu, amene adzaphwanya Satana ndi kuchotsa mavuto onse amene anabwera chifukwa cha kugalukira ndi kuchimwa kumene kunachitikako
Yehova analonjeza Abulahamu ndi Davide kuti adzakhala makolo a Mbewu kapena kuti Mesiya, amene adzalamulire monga Mfumu kwamuyaya
Yehova anauza aneneri kuti alosere zoti Mesiya adzathetsa uchimo ndi imfa. Monga Mfumu, Mesiyayo limodzi ndi olamulira anzake, adzalamulira mu Ufumu wa Mulungu umene udzathetse nkhondo, matenda ngakhalenso imfa
Yehova anatumiza Mwana wake padziko lapansi ndipo anam’dziwikitsa kuti ndi Mesiya. Yesu analalikira za Ufumu wa Mulungu ndipo anapereka moyo wake monga nsembe. Kenako Yehova anamuukitsa monga mzimu
Yehova anaika Mwana wake kukhala Mfumu kumwamba ndipo chimenechi chinali chiyambi cha masiku otsiriza a dziko loipali. Yesu amatsogolera otsatira ake akamalalikira za Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi
Yehova adzalamula Mwana wake kuti Ufumu wake uyambenso kulamulira padziko lapansi. Ufumuwu udzaphwanya maboma onse oipa, udzabweretsa Paradaiso, komanso mu ufumuwu, anthu onse okhulupirika adzakhala angwiro. Pa nthawiyi, zidzadziwika kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndipo dzina lake lidzayeretsedwa mpaka muyaya