ZAKUMAPETO C
Mmene Mungaphunzitsire ndi Buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale
Abale anapemphera kwambiri komanso kufufuza mozama kuti atulutse buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Kuti muthe kuligwiritsa ntchito bwino pophunzitsa, yesani kutsatira njira zotsatirazi.
Musanapite kuphunziro
-
1. Konzekerani mokwanira. Pochita zimenezi, ganiziraninso zomwe wophunzirayo akufunikira, mmene zinthu zilili pa moyo wake komanso zomwe amakhulupirira. Ganizirani mfundo zomwe angavutike kuzimvetsa ndi mmene mungamuthandizire. Onani mmene mfundo za m’mbali yakuti “Onani Zinanso,” zingamuthandizire. Ndipo muzikhala okonzeka kuzigwiritsa ntchito paphunzirolo.
Pochititsa phunziro
-
2. Yambani komanso malizani ndi pemphero ngati wophunzirayo wavomereza.
-
3. Yesetsani kuti musamalankhulepo kwambiri. Muzikambirana mfundo zomwe zili paphunzirolo ndipo muzimupatsa mpata wofotokozapo maganizo ake.
-
4. Mukamayamba gawo latsopano, werengani mawu ofotokozera ndipo tchulani maphunziro ena omwe ali m’gawolo.
-
5. Pomaliza gawo lililonse, muzigwiritsa ntchito mfundo zobwereza kuti muthandize wophunzirayo kukumbukira zomwe waphunzira.
-
6. Pokambirana phunziro lililonse ndi wophunzira wanu:
-
Muziwerenga ndime.
-
Muziwerenga malemba onse olembedwa kuti “Werengani.”
-
Mungawerengenso malemba ena omwe ali mu ndimezo ngati pakufunikira.
-
Onerani mavidiyo onse olembedwa kuti “Onerani” (ngati muli nawo).
-
Gwiritsani ntchito mafunso onse.
-
Muziuza wophunzira kuti azichita chidwi ndi zithunzi za m’gawo la “Fufuzani Mozama” n’kumupempha kuti aperekepo ndemanga.
-
Muzigwiritsa ntchito kabokosi kakuti “Zolinga” kuti wophunzira wanu aziona mmene akupitira patsogolo. Mungamulimbikitse kukwaniritsa cholinga chomwe wapatsidwa kapena kudziikira cholinga china kapenanso kukhala ndi zolinga zonse ziwiri.
-
Mufunseni ngati pali nkhani kapena vidiyo iliyonse m’chigawo cha “Onani Zinanso” yomwe yamusangalatsa pomwe amakonzekera phunzirolo.
-
Yesetsani kumaliza phunziro lililonse pa ulendo umodzi.
-
Pambuyo pa phunziro
-
7. Pitirizani kuganizira wophunzira wanu. Pemphani Yehova kuti adalitse wophunzira wanu chifukwa cha khama lake komanso kuti akupatseni nzeru zothandizira wophunzirayo.