Kukhululuka
Kodi Yehova ndi wofunitsitsa kukhululuka?
Onaninso 2Pe 3:9
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Sl 78:40, 41; 106:36-46—Yehova ankakhululukira anthu ake mobwerezabwereza ngakhale kuti zimene ankachitazo zinkamukhumudwitsa
-
Lu 15:11-32—Yesu anapereka fanizo losonyeza zimene Yehova amachita potikhululukira ndipo anafotokoza za bambo wachifundo yemwe anakhululukira mwana wake pambuyo poti walapa
-
Kodi Yehova anachita chiyani kuti azitikhululukira machimo?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Ahe 9:22-28—Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Khristu anakhetsa magazi ake imene ndi njira yokhayo yomwe imatithandiza kuti tikhululukidwe machimo
-
Chv 7:9, 10, 14, 15—Mtumwi Yohane anaona m’masomphenya “khamu lalikulu la anthu” omwe anali oyera pamaso pa Mulungu chifukwa chokhulupirira nsembe ya Yesu
-
Anthu ena akatilakwira, kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikufuna kuti Yehova azitikhululukira?
Mt 6:14, 15; Mko 11:25; Lu 17:3, 4; Yak 2:13
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Yob 42:7-10—Yehova asanachotsere Yobu mavuto ake komanso kumudalitsa, anamuuza kuti apempherere anzake atatu omwe ankalankhula zosalimbikitsa aja
-
Mt 18:21-35—Yesu anafotokoza nkhani yosonyeza kuti ngati tikufuna kuti Yehova atikhululukire, nafenso tizikhululukira anthu ena
-
N’chifukwa chiyani tifunika kuulula komanso kulapa moona mtima tikachimwa?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Sl 32:1-5; 51:1, 2, 16, 17—Davide anavutika kwambiri mumtima atachita machimo aakulu kenako analapa moona mtima
-
Yak 5:14-16—Yakobo ananena kuti ngati tachita tchimo lalikulu, tizifotokozera akulu
-
Kodi tiyenera kusintha zinthu ziti ngati tikufuna kuti Yehova atikhululukire?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
1Mf 21:27-29; 2Mb 18:18-22, 33, 34; 19:1, 2—Ahabu anamva chisoni Yehova atamuuza kuti amupatsa chilango koma anamuchitira chifundo. Komabe, iye sanasonyeze kudzichepetsa kuti walapa moona mtima, choncho sanamukhululukire ndipo anaphedwa
-
2Mb 33:1-16—Ngakhale kuti Manase anachita zoipa zambiri, atalapa Yehova anamukhululukira. Koma pambuyo pake anasintha, anathandiza Aisiraeli kusiya kulambira mafano n’kuyamba kulambira Yehova
-
Ngati talapa moona mtima, kodi Yehova angatikhululukire kufika pati?
Sl 103:10-14; Yes 1:18; 38:17; Yer 31:34; Mik 7:19
-
Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:
-
2Sa 12:13; 24:1; 1Mf 9:4, 5—Ngakhale kuti Davide anachita machimo aakulu kwambiri, Yehova anamukhululukira atalapa kenako anamutchula kuti ndi munthu wokhulupirika
-
Kodi Yesu anachita chiyani potengera chitsanzo cha Yehova pa nkhani yokhululukira ena mofunitsitsa?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Mt 26:36, 40, 41—Yesu atapeza ophunzira ake akugona pa nthawi yomwe iye ankafuna kuti akhale nawo limodzi, anawamvetsa ataona kuti atopa
-
Mt 26:69-75; Lu 24:33, 34; Mac 2:37-41—Petulo atamukana Yesu katatu kuti sakumudziwa, anamukhululukira atalapa. Kenako, Yesu ataukitsidwa anakaonekera kwa iye ndipo pambuyo pake anamugwiritsa ntchito mwapadera kuti athandize mipingo
-
Kodi timadziwa bwanji kuti si machimo onse amene Yehova amakhululuka?
Mt 12:31; Ahe 10:26, 27; 1Yo 5:16, 17
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Mt 23:29-33—Yesu anachenjeza alembi ndi Afarisi kuti adzaweruzidwa mwa kuponyedwa m’Gehena, kapena kuti chiwonongeko chotheratu
-
Yoh 17:12; Mko 14:21—Yesu anatchula Yudasi Isikarioti kuti “mwana wa chiwonongeko” ndipo ananena kuti zikanakhala bwino akanapanda kubadwa
-
N’chiyani chimene chingatithandize kuti tizikhululukira ena?