ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI
Tikuyesetsa Kuti Ntchito Yolalikira Padziko Lonse Izikhala Pamalo Oyamba
LACHITATU pa 23 September, 2015, Bungwe Lolamulira linalengeza za kusintha komwe kunachitika m’gulu la Yehova n’cholinga choti ndalama zimene abale amapereka zizigwiritsidwa ntchito pa zinthu zofunika kwambiri. Chilengezochi chinaperekedwa m’mabanja onse a Beteli. Kenako Loweruka pa 3 October, 2015, Bungwe Lolamulira linafotokoza bwinobwino za chilengezochi ndipo linati: “Lemba la Afilipi 1:10, limanena kuti ‘tizitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.’ Mogwirizana ndi malangizo anzeruwa, ifeyo [Bungwe Lolamulira] tikufuna kuika patsogolo ntchito yolalikira komanso ntchito zomwe zimathandiza kwambiri kuti abale akhale olimba mwauzimu.”
Kenako M’bale Stephen Lett, wa m’Bungwe Lolamulira, anafotokozanso za nkhaniyi papulogalamu ya JW Broadcasting. M’baleyu anati: “Bungwe Lolamulira likuganizira kwambiri za ntchito yolalikira. Choncho tayesa kupeza njira zochepetsera ndalama zimene zimagwiritsidwa ntchito m’maofesi a nthambi n’cholinga choti ndalama zambiri zizipita ku ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, ntchito zina zomwe zakhala zikuchitika pa Beteli kwa nthawi yaitali, zachepetsedwa kapenanso kuthetsedwa. Zimenezi zachititsa kuti chiwerengero cha anthu otumikira m’maofesi a nthambi chichepetsedwe.”
Kuchokera mu September 2015 abale ndi alongo okwana 5,500 omwe ankatumikira m’maofesi a nthambi, anauzidwa kuti azikagwira ntchito yolalikira. Abale ndi alongowa anafunika kusintha zambiri kuti ayambe utumiki watsopanowu. Komabe Yehova akuwadalitsa komanso anthuwa akuthandiza kwambiri pa ntchito yolalikira ndiponso kuphunzitsa.
Banja lina la ku Sri Lanka, lomwe linkatumikira pa Beteli, linauzidwa kuti lizikachita upainiya. Banjali linaona kuti uwu ndi mwayi wawo wosonyeza kuti amadalira kwambiri Yehova komanso gulu lake. Iwo anati: “Sitinkadziwa kuti zitithera bwanji. Koma sitinkakayikira zoti Yehova atithandiza. Choncho tinapemphera kuti, ‘Chonde Yehova, kaya tikumana ndi zotani, tithandizeni kuti tonse tizichita upainiya wokhazikika.’ M’mwezi woyamba titangochoka pa Beteli, tinali ndi ndalama zochepa kwambiri komanso tinalibe zinthu zina zofunikira. Koma timaona kuti Yehova anatisamalira kwambiri. Panopa tili pa ntchito komanso tikuchita upainiya. Timafunikanso kugwira ntchito
zapakhomo. Komabe zimene tinaphunzira ku Beteli zikutithandiza kuti tizitha kuchita zonsezi bwinobwino. Timaona kuti palibenso chinthu chosangalatsa kwambiri kuposa kuchita upainiya n’kumathandiza anthu kudziwa choonadi.”Abale ndi alongo ena omwe poyamba ankatumikira pa Beteli ya ku Colombia anaphunzira chinenero china ndipo anapita kukathandiza pa ntchito yolalikira kumadera akumidzi. Abale ndi alongowa athandizanso kwambiri mipingo imene asamukira. Mwachitsanzo, woyang’anira dera wina anafotokoza zokhudza banja lina limene linasamukira mumpingo wa m’dera lake. Iye anati: “Abale ndi alongo akuona kuti banjali lawathandiza kwambiri. Chiwerengero cha anthu omwe amalowa mu utumiki chawonjezeka ndipo abale akuphunzitsidwa kuti akhale ndi maudindo osiyanasiyana mumpingo.” Palinso abale ndi alongo ambiri amene poyamba ankatumikira pa Beteli koma panopa amangothandiza kwa tsiku limodzi kapena angapo pa mlungu.
M’bale wina yemwe anatumikira pa Beteli ya ku Japan kwa zaka 31, anauzidwa kuti akatumikire mumpingo wina womwe unali ndi akulu awiri okha kudera la Kumamoto. Mpingo womwe anatumizidwawo unkafunika kukonzanso Nyumba ya Ufumu yawo. M’baleyu atamva zimenezi anaganiza kuti asayambe msanga ntchito kuti akonze nawo Nyumba ya Ufumuyo. Koma ntchitoyi isanayambe, m’derali munachitika chivomerezi chachikulu. Popeza anali asanayambe ntchito, m’baleyu anagwira nawo ntchito yothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi chivomerezichi komanso kuchita maulendo aubusa. Iye anati: “Ndikaganizira zomwe zinachitikazi, ndimaona kuti Yehova ananditumiza kudera limene ankadziwa kuti kudzafunika thandizo lalikulu.”
M’bale Phil ndi mkazi wake Sugar, omwe ankatumikira pa Beteli ya ku Australasia, anati: “Titauzidwa kuti tisiye utumiki wa pa Beteli, tinagwirizana kuti tiyesetse kukhala moyo wosalira zambiri. Tinapempha Yehova kuti azitithandiza kusankha zochita mwanzeru komanso kuti azidalitsa zomwe tasankha. Tinkafunitsitsa kukatumikira kudziko lina. Timaona kuti Yehova wadalitsa zimene tinasankha ndipo watithandiza kuti tizimutumikira ndi mtima wonse.” Panopa banjali limasonkhana ndi kagulu ka mpingo wachingelezi komwe kali pachilumba cha Samal ku Philippines. Pachilumbapa pali ofalitsa 34 ndi apainiya 9. Banjali lili ndi mayina a anthu 120 achidwi ofunika kuwayendera. Iwo anati: “Izi zikusonyeza kuti pali ntchito yambiri yosangalatsa yoti tigwire. Timaona kuti tinachita bwino kudalira Yehova. Zimenezi zatithandiza kuti tizimukhulupirira komanso kumukonda kwambiri.”
Mlongo wina wosakwatiwa wa ku Russia, poyamba ankatumikira pa Beteli koma kenako anauzidwa kuti akachite upainiya wapadera. Mlongoyu anati: “Kuchita upainiya kwandithandiza kuti ndizikhala ndi nthawi yambiri yogwira ntchito yolalikira za Ufumu wa Mulungu. Ntchitoyi ndi yofunika kwambiri ndipo sidzabwerezedwanso. Ndimasangalala zedi kuti Yehova akundigwiritsa ntchito.” Panopa mlongoyu ali ndi maphunziro 6. Munthu wina amene amaphunzira naye ndi wa ku Iraq, wina wa ku Nigeria, wina wa ku Sri Lanka, wina wa ku Syria ndipo wina ndi wa ku Zambia.
Abale ndi alongo ambiri omwe ankatumikira pa Beteli ya ku Zambia anauzidwa kuti akachite upainiya wokhazikika. Abalewa akusangalala kwambiri chifukwa amakhala ndi nthawi yambiri yogwira ntchito yolalikira. M’bale Andrew amachita upainiya ndi mkazi wake ndipo anati: “Pasanapite nthawi yaitali titangochoka pa Beteli, tinathandiza
anthu awiri kudziwa kuwerenga ndi kulemba. Mnyamata wina yemwe timaphunzira naye Baibulo ali ndi zaka 10 ndipo posachedwapa ayamba kukamba nkhani pa misonkhano ya mkati mwa mlungu. Banja lina lomwe tinalilalikira linabwera pa Chikumbutso ndipo kuchokera nthawi imeneyo siliphonya misonkhano. Panopa banjali likupitirizabe kuphunzira Baibulo ndipo phunziro likuyenda bwino. Timaona kuti zonsezi zinatheka chifukwa choti tinatsatira malangizo a Yehova, tinkazindikira kuti akutithandiza komanso tinkakhulupirira kuti atidalitsa.”Edson ndi Artness nawonso ankatumikira pa Beteli ya ku Zambia koma anauzidwa kuti asiye utumikiwu. Pa nthawiyi n’kuti patangotha miyezi yochepa atakwatirana. Artness anati: “Zimene tinaphunzira pa Beteli zinatithandiza kuti tizigwiritsa ntchito mosamala ndalama zochepa zomwe tinali nazo. Zinatithandizanso kuti tikhalebe osangalala komanso kuti tisamakhale ndi ngongole. Sitinong’oneza bondo kuti tinasankha kutumikira pa Beteli. Taphunzira kuti ungathe kusintha utumiki umene unkaukonda n’kuyamba kuchita wina ndipo uyenera kudalira Yehova kuti akuthandize. Tikuona kuti panopa chikhulupiriro chathu chalimba ndipo tikufunitsitsa kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova.”