MUTU 8
Mukakumana ndi Mavuto Amwadzidzidzi
“Mukusangalala kwambiri ngakhale kuti padakali pano n’koyenera kuti muvutike kwa kanthawi chifukwa cha mayesero osiyanasiyana amene akukuchititsani chisoni.”—1 Petulo 1:6
Ngakhale mutayesetsa kwambiri kuti mukhale ndi banja losangalala, mukhoza kukumana ndi mavuto amwadzidzidzi. (Mlaliki 9:11) Koma Yehova amatikonda ndipo amatithandiza tikakumana ndi mavuto. Kutsatira mfundo zimene zili m’mutu umenewu kungathandize inuyo ndi banja lanu kuti mupirire mavuto ngakhale atakhala aakulu kwambiri.
1 MUZIDALIRA YEHOVA
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: ‘Muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Nthawi zonse muzikumbukira kuti Mulungu si amene amayambitsa mavuto anu. (Yakobo 1:13) Mukamayesetsa kukhala naye pa ubwenzi wabwino, adzakuthandizani kwambiri. (Yesaya 41:10) “Mukhuthulireni za mumtima mwanu.”—Salimo 62:8.
Kuwerenga ndiponso kuphunzira Baibulo tsiku lililonse kungakulimbikitseninso. Mukatero mudzaona umboni wakuti Yehova “amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:3, 4; Aroma 15:4) Iye amalonjeza kuti adzakupatsani “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afilipi 4:6, 7, 13.
ZIMENE MUNGACHITE:
-
Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuupeza mtima komanso kuganiza bwinobwino
-
Ganizirani njira zonse zimene mungatsatire ndiyeno n’kusankhapo imene ingakuthandizeni
2 MUZIDZISAMALIRA KOMANSO KUSAMALIRA BANJA LANU
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Mtima wa munthu womvetsa zinthu umadziwa zinthu, ndipo khutu la anzeru limafunafuna kudziwa zinthu.” (Miyambo 18:15) Muzikambirana ndi aliyense m’banjamo ndiponso kumvetsera bwino akamalankhula kuti mudziwe zimene angafunike.—Miyambo 20:5.
Kodi mungatani ngati wina m’banjamo kapena wachibale wamwalira? Musamachite manyazi kulira. Kumbukirani kuti ngakhale Yesu “anagwetsa misozi.” (Yohane 11:35; Mlaliki 3:4) Muyeneranso kupuma ndiponso kugona mokwanira. (Mlaliki 4:6) Zimenezi zingakuthandizeni kwambiri kuti mupirire.
ZIMENE MUNGACHITE:
-
Muzikambirana nthawi ndi nthawi ndi banja lanu. Mukatero, simudzavutika kukambirana momasuka mukakumana ndi mavuto amwadzidzidzi.
-
Muzilankhula ndi anthu ena amene akumana ndi vuto lofanana ndi lanu
3 LOLANI KUTI ENA AKUTHANDIZENI
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miyambo 17:17) Anzanu angafune kukuthandizani koma mwina sangadziwe zoti achite. Musachite manyazi kuwauza zimene mukufuna. (Miyambo 12:25) Muyeneranso kupempha anthu amene amadziwa bwino Baibulo kuti akupatseni malangizo chifukwa malangizowo angakuthandizeni kwambiri.—Yakobo 5:14.
Mukamakonda kucheza ndi anthu amene amakhulupirira Mulungu komanso malonjezo ake iwo adzakulimbikitsani kwambiri. Mudzalimbikitsidwanso mukamathandiza anthu ena amene akuvutikanso. Muziwauza zimene zimakuchititsani kukhulupirira Yehova ndiponso malonjezo ake. Muzilimbikira kuthandiza anthu ena komanso musasiye kucheza ndi anthu amene amakukondani.—Miyambo 18:1; 1 Akorinto 15:58.
ZIMENE MUNGACHITE:
-
Muzikambirana ndi mnzanu amene mumamudalira n’kulola kuti akuthandizeni
-
Musamubisire zimene mukufuna