N’chifukwa Chiyani Ndimaopa Kuuza Anzanga Akusukulu Zimene Ndimakhu Lupirira?
Mutu 17
N’chifukwa Chiyani Ndimaopa Kuuza Anzanga Akusukulu Zimene Ndimakhu Lupirira?
“Nthawi zina ndinkakhala ndi mwayi wofotokozera anzanga a kusukulu zimene ndimakhulupirira, koma sindinkafotokoza chilichonse.”—Anatero Kaleb.
“Nthawi ina aphunzitsi athu anauza aliyense kuti afotokoze zimene amadziwa pa nkhani yakuti anthu anachita kulengedwa kapena kusintha kuchokera ku zinyama. Ndinkadziwa ndithu kuti umenewu unali mwayi wanga wofotokoza zimene ndimakhulupirira. Koma ndinali ndi mantha kwambiri moti sindinanene kalikonse. Kenako ndinayamba kudziimba mlandu.”—Anatero Jasmine.
NGATI ndinu Mkhristu wachinyamata, n’kutheka kuti munakumanapo ndi zimene zinachitikira Kaleb ndi Jasmine. Mwina nanunso mumakonda kwambiri mfundo za m’Baibulo zimene mumaphunzira ndipo mumafuna mutamauzako anzanu. Koma mwina mumachita mantha. Kodi mungatani kuti muzilimba mtima? Tsatirani mfundo zili m’munsizi:
1. Dziwani chimene chimakuchititsani mantha. Mukamaganizira zofotokozera anthu ena zimene mumakhulupirira, n’zosavuta kuyamba kuganiza kuti anzanuwo akusekani. Koma nthawi zina kufotokoza kapena kulemba zimene zimakuchititsani mantha kungakuthandizeni kuti manthawo achepe.
Malizitsani chiganizo chotsatirachi:
● Chimene ndimaopa kuti chingachitike ndikamafotokozera anzanga a kusukulu zimene ndimakhulupirira ndi: ․․․․․
Dziwani kuti zimene mumaopazo ndi zimenenso achinyamata ena achikhristu amaopa. Mwachitsanzo, mnyamata wina wazaka 14, dzina lake Christopher, ananena kuti: “Ndimaopa kuti anzanga ayamba kundiseka komanso kumandinena.” Kaleb, yemwe tamutchula kumayambiriro uja, ananenanso kuti: “Ndinkaopa kuti wina andifunsa funso loti sindikudziwa yankho lake.”
2. Vomerezani kuti ndi mmene ziyenera kukhalira. Kodi tinganene kuti palibe chifukwa chochitira mantha? Ayi. Tikutero chifukwa cha zimene Ashley wazaka 20 ananena kuti: “Ana ena ankanamizira kuti akufuna kudziwa zimene ndimakhulupirira. Koma kenako ankatembenuza zimene ndanena n’kuyamba kundigemula pagulu.” Nicole wazaka 17 anafotokoza zimene zinamuchitikira kuti: “Mnyamata wina anayerekezera mawu a pavesi linalake m’Baibulo mwake ndi m’Baibulo mwanga n’kupeza *
kuti anali osiyana ndipo ananena kuti Baibulo langa linasinthidwa. Atanena zimenezi ndinasowa chonena.”Zinthu ngati zimenezi n’zochititsadi mantha. Koma m’malo mopewa kuti zimenezi zisachitike, vomerezani kuti ndi zimene ziyenera kuchitikira Mkhristu aliyense. (2 Timoteyo 3:12) Matthew wazaka 13 ananena kuti: “Yesu ananena kuti otsatira ake adzazunzidwa, choncho sitingayembekezere kuti aliyense angasangalale ndi zimene timakhulupirira.”—Yohane 15:20.
3. Ganizirani ubwino wake. Kodi zinthu zimene zikuoneka ngati zochititsa mantha zikhoza kukhala ndi zotsatira zabwino? Amber wazaka 21 amaona choncho. Iye anati: “N’zovuta kufotokoza mfundo zimene umakhulupirira kwa munthu amene sakhulupirira Baibulo, komabe kuchita zimenezi kumakuthandiza kuti umvetse bwino mfundo zimene umakhulupirirazo.”—Aroma 12:2.
Onaninso zimene munalemba kuti zimakuchititsani mantha pa mfundo yoyamba ija. Tsopano ganizirani ndi kulemba zinthu ziwiri zabwino zomwe zikhoza kuchitika ngati zimene mwalembazo zitachitikadi.
1 ․․․․․
2 ․․․․․
Dziwani izi: Kufotokozera anzanu zimene mumakhulupirira kukhoza kuthandiza kuti anzanuwo asamakunyengerereni kuchita Miyambo 23:15.
zinthu zoipa. Kufotokoza maganizo anu kungakuthandizeninso kuti muzikhala olimba mtima, muzikonda kwambiri Yehova Mulungu komanso kuti iyeyo azikukondani.—4. Muzikonzekera. Lemba la Miyambo 15:28 limati: “Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe.” M’malo mongoganizira zimene mukufuna munene, muziganiziranso mafunso amene anzanuwo akhoza kukufunsani. Fufuzani mfundo zokhudza nkhaniyo komanso konzekerani mfundo zimene mungakonde kukatchula poyankha anzanuwo.—Onani tchati cha mutu wakuti, “Konzekerani Zimene Mungayankhe” patsamba 127.
5. Pezani poyambira. Kodi mungayambe bwanji kufotokoza zimene mumakhulupirira? Pali njira zingapo. Kufotokozera ena zimene mumakhulupirira kuli ngati kusambira. Ena amalowa m’madzi pang’onopang’ono pomwe ena amangodumphiramo. Mukhoza kuyamba ndi nkhani zina zosakhala zachipembedzo, kenako n’kuyamba kuisintha nkhaniyo pang’onopang’ono. Koma ngati mukuona kuti mukuchita mantha kwambiri ndi zimene mnzanuyo akhoza Luka 12:11, 12) Andrew wazaka 17, ananena kuti: “Ndinkavutika kwambiri ndikamaganizira zofotokozera anthu ena zimene ndimakhulupirira kuposa mmene ndinkamvera ndikamafotokoza zinthuzo. Ndikayamba kukambirana ndi munthuyo ndinkaona kuti ndi zophweka kuposa mmene ndimaganizira.” *
kuchita, njira yabwino ingakhale kungofotokoza mfundozo kamodzin’kamodzi. (6. Muzichita zinthu mwanzeru. Solomo analemba kuti: “Aliyense wochenjera amachita zinthu mozindikira, koma wopusa amafalitsa uchitsiru.” (Miyambo 13:16) Munthu amene akufuna kusambira sangadumphire m’madzi omwe si akuya. Nanunso muyenera kusamala kuti musamangotsutsana pa zinthu zopanda phindu. Muzikumbukira kuti pali nthawi yolankhula ndi nthawi yokhala chete. (Mlaliki 3:1, 7) Ngakhalenso Yesu nthawi zina sankayankha mafunso.—Mateyu 26:62, 63.
Ngati mukufuna kumuyankha munthuyo ndi bwino kuyankha mwachidule komanso mosamala. Mwachitsanzo, ngati mnzanu atakufunsani kuti: ‘N’chifukwa chiyani susuta fodya?’ mungayankhe kuti: ‘Sindifuna kuwononga thupi langa.’ Mukhoza kupitiriza kumufotokozera za chikhulupiriro chanu kapena ayi potengera zimene iyeyo angayankhe.
Mfundo 6 zimene zafotokozedwa m’mutuwu zingakuthandizeni kukhala “okonzeka nthawi zonse kuyankha” za chikhulupiriro chanu. (1 Petulo 3:15) Komabe kukonzeka sikukutanthauza kuti simuzichita mantha. Alana wazaka 18, ananena kuti: “Ukafotokozabe zimene umakhulupirira ngakhale kuti uli ndi mantha, zimakupangitsa kusangalala poona kuti walimba mtima kuchita zinthu zimene mwina sizingathe bwino. Ndipo nkhaniyo ikatha bwino m’pamene umasangalala kwambiri chifukwa umaona kuti wasonyeza kulimba mtima.”
Kodi mumakhumudwa ndi zinthu zimene zimachitika kusukulu? Werengani nkhaniyi kuti muone zimene mungachite.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Anthu amene anamasulira mabaibulo anagwiritsa ntchito mawu osiyanasiyana. Koma omasulira ena anayesetsa kugwiritsa ntchito mawu olondola ogwirizana ndi zinenero zoyambirira zimene zinagwiritsidwa ntchito polemba Baibulo.
^ ndime 18 Onani bokosi lakuti, “Njira Zoyambira Kukambirana,” patsamba 124.
LEMBA
“Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.”—1 Petulo 3:15.
MFUNDO YOTHANDIZA
M’malo mowauza anzanuwo zimene ayenera kukhulupirira komanso zimene mukuona kuti n’zabodza, auzeni molimba mtima zimene inuyo mumakhulupirira komanso chimene chimakupangitsani kuona kuti zimene mumakhulupirirazo n’zolondola.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
N’kutheka kuti anzanu ena amakusirirani chifukwa choyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo nthawi zonse koma amachita manyazi kuti akufunseni zimene mumakhulupirira.
ZOTI NDICHITE
Mnzanga amene ndikhoza kumuuza zimene ndimakhulu pirira ndi [lembani dzina la mnzanuyo] ․․․․․
Nkhani imene ndikuganiza kuti angachite nayo chidwi kwambiri ndi ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani anzanu a kusukulu amanyoza zimene mumakhulupirira?
● Ngati mukufuna kuuza anzanu zimene mumakhulupirira, n’chifukwa chiyani ndi bwino kufotokoza zinthuzo molimba mtima?
[Mawu Otsindika patsamba 126]
Ndili wamng’ono sindinkafuna kuchita zinthu zosiyana ndi zimene anzanga ankachita. Koma kenako ndinayamba kusangalala pozindikira kuti zinthu zimene ndimakhulupirira zimandithandiza kuti ndikhale ndi moyo wabwino. Kuzindikira zimenezi kunandithandiza kuti ndizinyadira chikhulupiriro changa.”—Anatero Jason
[Bokosi patsamba 124]
Njira Zoyambira Kukambirana
● “Nthawi ya holide uzipanga chiyani?” [Akayankha, muuzeni zinthu zauzimu zimene mukufuna kuchita monga kupita kumsonkhano kapena kuwonjezera utumiki.]
● Mufunseni ngati wamva nkhani imene mwawerenga munyuzipepala kapena imene mwamva pawailesi, kenako mufunseni kuti: “Kodi iweyo maganizo ako ndi otani pa nkhani imeneyi?”
● “Kodi ukuganiza kuti mavuto a zachuma [kapena mavuto ena] adzatha? [Mudikireni ayankhe.] N’chifukwa chiyani ukuona choncho?”
● “Umapemphera tchalitchi chanji?”
● “Kodi uli ndi mapulani otani kutsogoloku?” [Akayankha, muuzeni zolinga zanu zauzimu.]
[Tchati patsamba 127]
(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)
Zoti Muchite
Konzekerani Zimene Mungayankhe Koperani
Maganizo: Kambiranani tchatichi ndi makolo anu komanso achinyamata anzanu a kumpingo. Malizitsani kulemba tchatichi. Kenako ganizirani mafunso ena amene anzanu a kusukulu angafunse ndipo lembani mmene mungawayankhire.
Funso Yankho Funso lina Yankho
N’chifukwa chiyani → Ndimalikonda → Ndiye kuti → Ayi, ndipo
Kusalowerera suchitira sawatcha koma sungamenye a Mboni za Yehova
ndale mbendera? Ndiye sindimalilambira. nkhondo mamiliyoni
kuti sumakonda poteteza ambirimbiri
dziko lako? dziko lako? amene ali
m’mayiko ena
sangamenyanenso
ndi dziko lathu.
N’chifukwa chiyani → Ndimaona kuti → Nanga bwanji → ․․․․․
mumakana kuthiridwa kuikidwa magazi utadziwa kuti
magazi? kukhoza kuchitits umwalira ukapanda
a munthu kutenga kuikidwa magazi?
matenda ngati Mulungu
a EDZI ndi sangakukhululukire
matenda ena. utaikidwabe?
Koma olo
Magazi nditadziwa kuti
m’magazimo mulibe
matendawo,
sindingalolebe
kuikidwa magazi
chifukwa Baibulo
limanena kuti
tizipewa magazi.
Ndiye ndimatsatira
mfundo imeneyi.
Ndinaonapo → Timangophunzitsidwa → Koma m’mesa → ․․․․․
anthu ena zimene Mulungu anthu a mpingo
a tchalitchi amafuna ndipo umodzi amayenera
chanuchi sitimakakamizidwa kuyendera mfundo
Zosankha akupanga kutsatira mfundozo. zofanana?
zakutizakuti. Aliyense ali ndi
Nanga bwanji ufulu wotsatira
iweyo sumachita zimene timaphunzira
zimenezi? kapena ayi.
N’chifukwa chiyani → Ndikhulupirira → ․․․․․ → ․․․․․
sumakhulupirira bwanji pamene
Chilengedwe zoti zamoyo asayansi eniakewo
zinachita kusintha amasiyananso
kuchokera ku maganizo pa
zinthu zina? nkhaniyi?
Iwowo monga
akatswiri anayenera
kumanena zofanana.
[Chithunzi patsamba 125]
Kufotokozera ena zimene mumakhulupirira kuli ngati kusambira. Ena amalowa m’madzi pang’onopang’ono, pomwe ena amangodumphiramo