Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Ngati Ndimapanikizika Kwambiri Kusukulu?

Kodi Ndingatani Ngati Ndimapanikizika Kwambiri Kusukulu?

Mutu 18

Kodi Ndingatani Ngati Ndimapanikizika Kwambiri Kusukulu?

“Ndinkapanikizika kwambiri ndikakhala kusukulu moti nthawi zambiri ndinkalakalaka nditangoyamba kulira.”​—Anatero Sharon.

“Kupanikizika ndi zochita za kusukulu sikutha ngakhale ukamakula. Chimene chimasintha ndi zinthu zimene zimakupangitsa kupanikizikazo.”​—Anatero James.

KODI mumaona kuti makolo anu samvetsa kuti mumapanikizika kwambiri mukakhala kusukulu? Mwina amanena kuti n’zosatheka kuti muzipanikizika chifukwa mulibe ngongole zoti mubweze, mulibe banja loti mulisamalire komanso simuli pa ntchito. Koma n’kutheka kuti mumaona kuti mumapanikizika mofanana ndi mmene makolo anu amapanikizikira, mwinanso kuwaposa.

Zinthu zina zimene zimapangitsa kuti muzipanikizika ndi zimene zimachitika munjira popita kapena pobwera kusukulu. Tara, yemwe amakhala ku United States, ananena kuti: “M’basi imene tinkakwera popita kusukulu, simunkachedwa kuyambika ndewu. Ndewu ikabadwa dalaivala ankaimitsa basiyo ndipo aliyense ankatsika kaye. Zimenezi zinkachititsa kuti tichedwe kwambiri.”

Kodi kupanikizikaku kumatha mukafika kusukulu? Ayi. Mwina mumakumananso ndi zinthu zotsatirazi:

Zochita za aphunzitsi.

“Aphunzitsi anga amafuna kuti ndizikhoza bwino m’kalasi ndiye ndimapanikizika kwambiri pofuna kuwasangalatsa.”​Anatero Sandra.

“Aphunzitsi ambiri amakakamiza ana kuti aziyesetsa kuti adzakhoze bwino mayeso, makamaka ngati anawo ali anzeru.”​Anatero April.

“Ngakhale zinthu zimene ukufuna kudzachita ukadzamaliza sukulu zitakhala zabwino, aphunzitsi ena amakupangitsa kuti uziona ngati ndiwe wachabechabe ngati zolinga zakozo zikusiyana ndi zimene iwowo akufuna kuti udzachite.” *​—Anatero Naomi.

Fotokozani mmene mumapanikizikira chifukwa cha zochita za aphunzitsi.

․․․․․

Zochita za anzanu.

“Ana a ku sekondale amakhala ndi ufulu wambiri ndipo amachita zinthu zambiri zosokonekera. Ngati sukuchita nawo zimene akuchitazo, amakutenga ngati wotsalira.”​Anatero Kevin.

“Tsiku lililonse ndimakumana ndi zinthu zimene zikhoza kundichititsa kuti ndimwe mowa komanso ndigonane ndi mtsikana. Nthawi zina ndi zovuta kudziletsa kuti usachite nawo zimene anzako akuchita.”​Anatero Aaron.

“Mmene ndakwanitsa zaka 12 anzanga ambiri amandinyengerera kuti ndipeze chibwenzi. Aliyense kusukulu amangondifunsa kuti: ‘Kodi iwe nde chibwenzi udzapeza liti?’”​—Anatero Alexandria.

“Anzanga ankandikakamiza kuti ndiyambe chibwenzi ndi mnyamata winawake. Nditakana anayamba kundinena kuti ndimafuna kumagonana ndi akazi anzanga. Ndipotu zimenezi zinkachitika ndili ndi zaka 10 zokha.”​Anatero Christa.

Fotokozani mmene mumapanikizikira chifukwa cha zochita za anzanu.

․․․․․

Zinthu zina. Ikani chizindikiro ichi ✔ pa zinthu zimene zimakupanikizani kwambiri kapena lembani m’munsimu.

□ Kukonzekera mayeso

□ Kufunitsitsa kuti muzikhoza bwino kwambiri

□ Homuweki

□ Kutizidwa kapena kuvutitsidwa ndi anyamata

□ Kuyesetsa kuti mukhoze ngati mmene makolo anu akufunira

□ Zina ․․․․․

Zimene Zingakuthandizeni Kuti Musamapanikizike Kwambiri

N’zosatheka kumaliza sukulu popanda kukumana ndi mavuto amene takambiranawa. Komabe n’zoona kuti kupanikizika kwambiri kumasowetsa mtendere. N’chifukwa chake mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Kuponderezedwa kumapangitsa munthu wanzeru kuchita zinthu zopanda nzeru.” (Mlaliki 7:7) Koma musalole kuti zimenezi zikuchitikireni. Chinsinsi chake ndi kuphunzira zoyenera kuchita mukapanikizika.

Kulimbana ndi vuto la kupanikizika kuli ngati kunyamula maweti. Munthu wonyamula maweti amayenera kukonzekera kuti zinthu zimuyendere bwino. Samalumikiza zitsulo zambirimbiri zomwe sangakwanitse kunyamula ndipo amayesetsanso kunyamula zitsulozo moyenera. Kuyesetsa kuchita zimenezi kumathandiza kuti asavulale. Koma ngati atapanda kuchita zimenezi akhoza kuvulala mwinanso kuthyoka kumene.

Mofanana ndi zimenezi, pamene mwapanikizika, n’zothekabe kumaliza bwinobwino ntchito imene muli nayo popanda kudzivulaza. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Chitani zinthu zotsatirazi:

1. Dziwani zimene zimayambitsa kupanikizika. Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Koma kuti mubisale, muyenera kudziwa kaye chimene chimayambitsa vutolo. Onaninso malo amene munaika zizindikiro aja. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimakupanikizani kwambiri?

2. Fufuzani. Mwachitsanzo, ngati mukuona kuti mukumapanikizika ndi homuweki, fufuzani mfundo zopezeka m’Mutu 13, m’Buku Lachiwiri. Ngati mumavutika ndi maganizo ofuna kugonana ndi mnzanu wa m’kalasi, mungapeze mfundo zothandiza  . Ngati mumavutika ndi maganizo ofuna kugonana ndi mnzanu wa m’kalasi, mungapeze mfundo zothandiza  . Ngati mumavutika ndi maganizo ofuna kugonana ndi mnzanu wa m’kalasi, mungapeze mfundo zothandiza m’Mutu 2, 5 ndi 15, m’Buku Lachiwiri.

3. Musazengereze. Mavuto ena amachepa mukangowasiya osachitapo kanthu. Koma nthawi zambiri zimenezi zimachititsa kuti mavutowo azingokulirakulira kenako mumapanikizika. Mukapeza njira yothetsera vuto linalake musamazengereze. Muzithana ndi vutolo nthawi yomweyo. Mwachitsanzo, ngati ndinu wa Mboni za Yehova ndipo mukufuna muzitsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wanu, mungachite bwino kudzidziwikitsa mwamsanga. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamapanikizike kwambiri. Marchet wazaka 20 ananena kuti: “Chaka chilichonse tikamatsegulira sukulu, ndinkayesetsa kuyamba kukambirana ndi anzanga nkhani inayake n’cholinga choti ndifotokoze zimene ndimakhulupirira. Ndinkaona kuti ndikachedwa kudzidziwikitsa kuti ndine wa Mboni, m’pamene anzanga ankandikakamiza kwambiri kuti ndichite zoipa. Kuchita zimenezi kunkandithandiza kuti ndizitsatira zimene ndimakhulupirira pa nthawi yonse imene ndinali kusukulu.”

4. Pemphani ena kuti akuthandizeni. Anthu amene anazolowera kunyamula maweti amakhala ndi malire a zitsulo zimene anganyamule. Inunso muli ndi malire a zimene mungakwanitse kuchita. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti palibe angakuthandizeni. (Agalatiya 6:2) Mukhoza kupempha makolo anu kapena Mkhristu wina amene mukuona kuti angakuthandizeni. Aonetseni zimene mwalemba kumayambiriro kwa mutuwu ndiyeno afunseni maganizo awo.

Kodi Kupanikizika N’kwabwino?

Mwina simungakhulupirire, koma ngati mumamva kupanikizika ndiye kuti zili bwino. Tikutero chifukwa kupanikizikako kumasonyeza kuti ndinu wakhama komanso kuti chikumbumtima chanu chikugwira ntchito bwinobwino. Onani mmene Baibulo limafotokozera munthu amene samapanikizika n’komwe: “Kodi ugonabe mpaka liti, waulesiwe? Udzuka nthawi yanji kutulo tako? Ukapitiriza kugona pang’ono, ukapitiriza katulo pang’ono, ukapitiriza kupinda manja pang’ono pogona, umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba, ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.”​—Miyambo 6:9-11.

Heidi yemwe ali ndi zaka 16 ananena kuti: “Kusukulu kungaoneke ngati simalo abwino koma mavuto amene amakupangitsani kupanikizika mukakhala kusukulu ndi amenenso mudzakumane nawo mukadzayamba ntchito.” N’zoona kuti kupanikizika sikuzolowereka. Koma ngati mutadziwa zoyenera kuchita, kupanikizikako kukhoza kukuthandizani kukhala munthu wolimba m’malo mokuvulazani.

M’MUTU WOTSATIRA

Ngati mukukumana ndi mavuto kusukulu, kodi ndi bwino kungoisiya?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Kuti mudziwe zambiri werengani Mutu 20.

LEMBA

‘Muzimutulira Mulungu nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’​—1 Petulo 5:7.

MFUNDO YOTHANDIZA

Gawani mavuto amene amakuchititsani kupanikizika m’magulu awiri. Gulu loyamba likhale la mavuto amene mukhoza kuwathetsa ndipo lachiwiri likhale la mavuto amene simungathe kuwathetsa. Choyamba, limbanani ndi mavuto amene mukhoza kuwathetsa. Sibwino kuwononga nthawi yanu kuganizira kwambiri za mavuto amene simungawathetse.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Kugona mokwanira usiku uliwonse, maola osachepera 8, kungakuthandizeni kuti musamapanikizike komanso kuti muzikumbukira zinthu mosavuta.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndisamapanikizike kwambiri ndi bwino kuti ngati n’zotheka ndizipita kukagona nthawi ikakwana ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi kufunitsitsa kuti muzipanga zinthu zonse molondola kungachititse bwanji kuti muzipanikizika kwambiri?

● Ngati mutapanikizika kwambiri, kodi mungalankhule ndi ndani?

[Mawu Otsindika patsamba 132]

“Tsiku lililonse bambo anga ankapemphera nane asanakandisiye kusukulu. Zimenezi zinkandithandiza kuti ndiziona kuti ndine wotetezeka.”​—Anatero Liz

[Chithunzi patsamba 131]

Kunyamula maweti moyenerera kungamuthandize munthu kukhala ndi thupi lamphamvu. Nakonso kuchita zinthu moyenera polimbana ndi kupanikizika kungathandize munthu kukhala ndi maganizo abwino