Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Msonkhano umene unachitika ntchito yathu italetsedwa. Ena mwa anthuwa ankamvetsera msonkhanowu ali m’boti

INDONESIA

Anatsimikiza Mtima Kuti Sabwerera M’mbuyo

Anatsimikiza Mtima Kuti Sabwerera M’mbuyo

Ntchito yolalikira italetsedwa ku Indonesia, abale a ku ofesi ya nthambi anakonza zoti ntchitoyi isaimiretu. M’bale Ronald Jacka ananena kuti: “Tinasamutsa mafailo athu achinsinsi, mabuku komanso ndalama n’kukaziika kunyumba zosiyanasiyana zomwe zinali zotetezeka mumzinda wa Jakarta. Kenako tinasamutsa ofesi ya nthambi n’kupita kumalo omwe anthu sakanawadziwa. Zitatero tinagulitsa nyumba zomwe zinali ofesi ya nthambi zija.”

Abale ambiri m’dzikoli anapitirizabe kuchita zinthu zauzimu komanso sankachita mantha. Ngakhale ntchito yathu isanaletsedwe, abalewa ankakumana ndi mavuto ambiri, koma anapitirizabe kudalira Yehova. Koma nthawi zina apolisi akapeza abale akulalikira, abale ena ankachita mantha kwambiri moti akulu ena anasainira zikalata zoti asiya kulalikira. Abale ena anaulula mayina a abale awo kwa apolisi. Zimenezi zitachitika, a ku ofesi ya nthambi anatumiza abale olimba mwauzimu kuti akalimbikitse mipingo komanso amene anasainira zikalata aja. Nayenso M’bale John Booth, yemwe anali m’Bungwe Lolamulira, anapita ku Indonesia ndipo anapereka malangizo olimbikitsa kwambiri kwa abale ndi alongo.

Apatu zinali zoonekeratu kuti Yehova ankalimbikitsa komanso kutonthoza anthu ake. (Ezek. 34:15) Nawonso akulu anayamba kuthandiza abale ndi alongo kuti azikonda kwambiri Mulungu. Zimenezi zinachititsa kuti ofalitsa apeze njira zina zolalikirira kuti asagwidwe. (Mat. 10:16) Abale ambiri anagula Baibulo lotsika mtengo ku bungwe loona za Mabaibulo la Indonesian Bible Society n’kumagawira kwa anthu amene ankaphunzira nawo. Abale ena ankathothola m’mabuku athu pepala limene pankalembedwa zokhudza amene amafalitsa mabukuwo ndipo akatero ankawagawira kwa anthu omwe asonyeza chidwi. Apainiya ambiri anapitirizabe kulalikira ndipo ankanamizira kuti akugulitsa malonda kunyumba ndi nyumba. Zimenezi zinali zofanananso ndi zimene abale ena anachitapo m’mbuyomo pa nthawi imene dziko la Japan linkalamulira dzikoli.

M’bale Norbert ndi Mlongo Margarete Häusler

Pofika mu 1977, akulu a ku nthambi yoona za ufulu wa zipembedzo anapezanso njira ina yothetsera ntchito ya a Mboni. Iwo anakana kuperekanso mapepala olola amishonale a Mboni za Yehova kukhalabe m’dzikolo. Zimenezi zinachititsa kuti amishonale ambiri awatumize m’mayiko ena. * M’bale Norbert Häusler, yemwe ankatumikira ndi mkazi wake Margarete mumzinda wa Manado, ananena kuti: “Abale ndi alongo ambirimbiri anabwera kubwalo la ndenge kudzatsanzikana nafe. Titakwera masitepe olowera m’ndenge, n’kufika pakhomo la ndengeyo, tinaima kaye n’kuyang’ana m’mbuyo. Tinaona abale ndi alongo ambirimbiri akutibayibitsa komanso akutilirira. Ankafuulanso kuti: ‘Muyende bwino! Muyende bwino!’ Titalowa m’ndengeyo nafenso tinayamba kulira.”

Abale Anazunzidwa Koopsa Pachilumba cha Sumba

Anthu ambiri anayamba kudziwa zoti a Mboni analetsedwa kugwira ntchito yawo m’dzikoli. Zitatero, akuluakulu a bungwe la mgwirizano wa matchalitchi ku Indonesia anauza mamembala onse a m’bungweli kuti auze anthu m’matchalitchi awo kuti azikanena ku polisi akaona wa Mboni aliyense akulalikira. Zimenezi zinachititsa kuti abale ayambe kumangidwa komanso kufunsidwa mafunso ndi apolisi m’zilumba za m’dzikoli.

Tsiku lina mkulu wa asilikali mumzinda wa Waingapu, womwe uli pachilumba cha Sumba, anaitanitsa abale 23 kuti akaonekere kumalo a asilikali a m’deralo. Abalewa atafika anawalamula kuti asainire chipepala chosonyeza kuti asiya chikhulupiriro chawo. Koma abalewa sanalole zimenezi ndipo mkulu wa asilikali uja anawalamula kuti abwerenso tsiku lotsatira. Abalewa anayenda wapansi mtunda wa makilomita 14 kupita ndi kubwera.

Abalewa atapita kukaonera tsiku lotsatira, anayamba kuwaitana mmodzimmodzi n’kumawakakamiza kuti asainire chipepala chija. Akakana, asilikaliwo ankawamenya ndi mtengo waminga. Asilikaliwo ankamenya abalewa mwankhanza kwambiri moti ena anakomoka. Pamene ankachita zimenezi n’kuti abale ena akungoyembekezera kuti nawonso amenyedwe. Itakwana nthawi yoti M’bale Mone Kele asainire chikalata chija, m’baleyu anapitadi n’kusainira. Zimenezi zinadabwitsa abale enawo. Koma m’baleyu anali atalemba kuti: “Ndidzakhalabe wa Mboni za Yehova mpaka kalekale.” Pamenepo mkulu wa asilikaliyo anapsa mtima kwambiri. M’bale Kele anamenyedwa koopsa moti anakagonekedwa m’chipatala koma sanasiye chikhulupiriro chake.

Mkulu wa asilikaliyu anachita zinthu zankhanzazi kwa masiku 11 n’cholinga choti abalewa asiye zimene amakhulupirira. Anawalamula kuti aimirire tsiku lonse padzuwa lotentha kwambiri. Anawakakamizanso kuti akwawe mtunda wa makilomita angapo komanso kuti azithamanga atanyamula katundu wolemera. Kenako anawalozetsa mpeni pakhosi n’kuwalamula kuti achitire sailuti mbendera, koma abalewa anakana. Zitatero anangolamula kuti amenyedwenso.

Abalewa ankapita m’mawa uliwonse kukaonekera kumalo a asilikaliwa ndipo tsiku lililonse sankadziwa kuti akakumana ndi zotani. Ali m’njira ankapemphera pamodzi komanso kulimbikitsana kuti akhalebe okhulupirika. Madzulo alionse ankabwerera kwawo atamenyedwa ndiponso ali magazi okhaokha koma ankasangalala kuti akhalabe okhulupirika kwa Yehova.

Abale a ku ofesi ya nthambi atadziwa kuti abalewa akuzunzidwa, nthawi yomweyo analemba makalata osonyeza kusagwirizana ndi zimene mkulu wa asilikaliyu ankachita. Makalatawa anapita kwa mkulu wa asilikali m’dera lonse la mzinda wa Timor, kwa mkulu wa asilikali m’chigawo chonse cha mzinda wa Bali, kwa woyang’anira asilikali mumzinda wa Jakarta komanso kwa akuluakulu aboma osiyanasiyana. Ataona kuti anthu adziwa zinthu zankhanza zimene ankachitazi, mkulu wa asilikali wa ku Waingapu uja anachita manyazi ndipo anasiya kuzunza abalewa.

“A Mboni za Yehova Ali Ngati Misomali”

M’zaka zotsatira, a Mboni za Yehova ambiri ku Indonesia anamangidwa, kufunsidwa mafunso ndi apolisi komanso kuchitidwa zinthu zankhanza. M’bale Bill Perrie ananena kuti: “M’dera lina, abale ambiri anawamenya n’kuwachotsa mano apatsogolo. Ndiye abale ankati akakumana ndi m’bale yemwe anali adakali ndi mano onse, ankamufunsa moseka kuti: ‘Kodi mwaphunzira kumene choonadi eti? Kapena anzathu munasaina chikalata chija?’ Ngakhale kuti abalewa anakumana ndi mavuto ambiri, anapitirizabe kusangalala komanso kutumikira Yehova mwakhama.”

“Nthawi imene ndinakhala m’ndende ndinaphunzira kudalira Yehova komanso ndinayamba kumukonda kwambiri”

Pa nthawi ina, a Mboni okwana 93 analamulidwa kukhala m’ndende kwa miyezi iwiri ndipo ena mpaka zaka 4. Mavuto amene anakumana nawo anawathandiza kukhala okhulupirika kwa Yehova. Mwachitsanzo, M’bale Musa Rade, atakhala m’ndende kwa miyezi 8, anayendera abale ndi alongo a m’dera limene ankakhala ndipo anawalimbikitsa kuti apitirize kugwira ntchito yolalikira. Iye anati: “Nthawi imene ndinakhala m’ndende ndinaphunzira kudalira Yehova komanso ndinayamba kumukonda kwambiri.” Anthu enanso amene ankaona zimene a Mboni anakumana nazo ananena kuti: “A Mboni za Yehova ali ngati misomali. Akamakhomedwa kwambiri m’pamenenso amalimba.”

Abale ndi alongo akupita kukalalikira m’tauni ya Ambon ku Maluku

^ ndime 1 Pa nthawiyi, M’bale Peter Vanderhaegen ndi M’bale Len Davis, omwe anachita umishonale kwa zaka zambiri m’dzikoli, anali atapitirira zaka 60, moti dziko la Indonesia silinkawaonanso ngati amishonale. Komanso Mlongo Marian Tambunan (yemwe poyamba anali Marian Stoove) anali atakwatiwa ndi mwamuna wa ku Indonesia konko. Choncho anthu atatu onsewa analoledwa kukhalabe m’dzikoli. Onse anakhalabe okhulupirika ndipo ngakhale kuti ntchito yolalikira inali yoletsedwa, anthuwa sanasiye kulalikira.