Mawu Oyamba
Baibulo Lopatulika lili ndi uthenga umene Mulungu analembera anthufe. Choncho timafunika kuliphunzira kuti timudziwe bwino amene analilemba. (Yohane 17:3; 2 Timoteyo 3:16) Kudzera mʼBaibulo, Yehova Mulungu anafotokoza cholinga chake kwa anthu komanso dziko lapansi.—Genesis 3:15; Chivumbulutso 21:3, 4.
Baibulo ndi buku lokhalo lomwe limathandiza anthu ambiri kusintha moyo wawo. Limatithandizanso kukhala ndi makhalidwe amene Yehova ali nawo monga chikondi, chifundo komanso kuganizira ena. Baibulo limatipatsa chiyembekezo chomwe chimatithandiza kupirira ngakhale titakumana ndi mavuto aakulu. Komanso limatithandiza kudziwa zinthu zimene zikuchitika mʼdzikoli zomwe sizigwirizana ndi zimene Mulungu amafuna.—Salimo 119:105; Aheberi 4:12; 1 Yohane 2:15-17.
Poyambirira, Baibulo linalembedwa mʼChiheberi, mʼChiaramu ndi mʼChigiriki. Baibulo lonse lathunthu kapena mbali yake, lamasuliridwa mʼzilankhulo zoposa 3,000. Kuyambira kale, Baibulo ndi buku lokhalo lomwe lamasuliridwa mʼzilankhulo zambiri komanso kufalitsidwa kwambiri. Zimenezitu nʼzosadabwitsa chifukwa ulosi wina wa mʼBaibulo umanena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu [womwe ndi uthenga wofunika kwambiri wa mʼBaibulo] udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.
Choncho poganizira kufunika kwa uthenga umene uli mʼBaibulo, tinaona kuti ndi bwino Baibuloli likonzedwenso kuti ligwirizane ndi uthenga wake womwe ndi wofunika kwambiri. Tinaona kuti tili ndi udindo waukulu womasulira uthenga wake molondola. Baibulo lokonzedwansoli, lamasuliridwa kuchokera ku Mabaibulo a Chingelezi a Dziko Latsopano a Malemba Opatulika amene akhala akutulutsidwa mʼmbuyomu. Baibulo loyamba la Chingelezi linatulutsidwa zaka zoposa 60 zapitazo. Koma pofika pano, mawu ambiri a Chingelezi asintha. Kusinthaku nʼkumene kunachititsa Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano, kuona kuti mʼpofunika kuti Baibuloli likonzedwenso. Nthawi zonse, cholinga chathu chimakhala kutulutsa Baibulo logwirizana ndi zomwe zili mʼmipukutu yoyambirira, lomveka bwino komanso losavuta kuwerenga. Mʼgawo la Zakumapeto muli nkhani zokhudza “Malamulo Omasulirira Baibulo,” “Zimene Zili MʼBaibuloli” komanso “Zimene Zinachitika Kuti Baibulo Lisungike Mpaka Lero.” Nkhanizi zikufotokoza zinthu zina zomwe zakonzedwanso mʼBaibuloli.
Anthu amene amakonda Yehova Mulungu komanso kumulambira, amafunika Baibulo lolondola ndi losavuta kumva. (1 Timoteyo 2:4) Zimenezi ndi zomwe zinachititsa kuti Baibulo la Chingelezi likonzedwenso nʼcholinga choti limasuliridwenso mʼzilankhulo zina zambiri. Choncho tili ndi chikhulupiriro ndiponso ndi pemphero lathu kuti mukamawerenga Baibulo la Malemba Opatulika limeneli, likuthandizeni pamene mukuyesetsa ‘kufunafuna Mulungu ndi kumupezadi.’—Machitidwe 17:27.
Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano
August 2013
Baibulo la Dziko Latsopano la Chichewa linatulutsidwa koyamba mu 2010. Ndipo Baibulo la Chichewali lakonzedwanso potengera zonse zimene zili mu Baibulo la Chingelezi la Dziko Latsopano, lokonzedwanso mu 2013.