Wolembedwa ndi Yohane 20:1-31
20 Tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya wa ku Magadala anapita kumandako* mʼmawa kwambiri,+ kudakali mdima, ndipo anaona kuti mwala wachotsedwa kale pamandawo.*+
2 Choncho anathamanga kupita kwa Simoni Petulo ndi kwa wophunzira wina, amene Yesu ankamukonda kwambiri uja.+ Iye anawauza kuti: “Ambuye awachotsa mʼmanda*+ muja, ndipo sitikudziwa kumene awaika.”
3 Atatero Petulo ndi wophunzira wina uja ananyamuka kupita kumandako.
4 Onse awiri anayambira limodzi kuthamanga, koma wophunzira winayo ankathamanga kwambiri kuposa Petulo ndipo anali woyambirira kukafika kumandako.
5 Atawerama nʼkusuzumira mkatimo, anaona nsalu zili pansi,+ koma sanalowemo.
6 Kenako Simoni Petulo amene ankabwera mʼmbuyo mwake anafikanso, ndipo analowa mʼmandamo. Mmenemo anaona nsalu zija zili pansi.
7 Nsalu imene anamukulungira kumutu sinaikidwe pamodzi ndi nsalu zina zija, koma anaipindapinda nʼkuiika payokha.
8 Kenako wophunzira amene anayambirira kufika kumanda uja analowanso mkatimo, ndipo anaona nʼkukhulupirira zimene anauzidwa.
9 Iwo anali asanamvetse zimene malemba amanena kuti Yesu ayenera kuuka kwa akufa.+
10 Choncho ophunzirawo anabwerera kunyumba kwawo.
11 Koma Mariya anatsala atangoima panja pafupi ndi mandawo, akulira. Akulira choncho, anawerama kuti aone mʼmandamo
12 ndipo anaona angelo awiri+ amene anavala zoyera atakhala pamene panali mtembo wa Yesu. Mmodzi anakhala pansi kumutu ndipo wina anakhala kumiyendo.
13 Iwo anamufunsa kuti: “Mayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?” Mayiwo anawayankha kuti: “Atenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene awaika.”
14 Atanena zimenezi, anatembenuka ndipo anaona Yesu ataima pamenepo, koma sanamuzindikire kuti ndi Yesu.+
15 Yesu anafunsa mayiyo kuti: “Mayi iwe, nʼchifukwa chiyani ukulira? Kodi ukufuna ndani?” Poganiza kuti ndi amene ankasamalira mundawo, iye anamuyankha kuti: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika ndipo ine ndikamutenga.”
16 Yesu anamuuza kuti: “Mariya!” Iye anatembenuka nʼkumuuza mʼChiheberi kuti: “Rab·boʹni!” (kutanthauza kuti “Mphunzitsi!”)
17 Yesu anamuuza kuti: “Usandikangamire chifukwa nthawi yoti ndipite kwa Atate sinakwane. Koma pita kwa abale anga+ ndipo ukawauze kuti, ‘Ine ndikupita kwa Atate wanga+ ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga+ ndi Mulungu wanu.’”
18 Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzirawo ndipo anawauza kuti: “Ambuye ndawaona ine!” Ndipo anawauza zimene Yesu anamuuza zija.+
19 Madzulo a tsiku limenelo, limene linali tsiku loyamba la mlungu, ophunzirawo anasonkhana pamodzi. Mʼnyumba imene anasonkhanayo anakhoma zitseko chifukwa ankaopa Ayuda. Koma Yesu analowa nʼkuima pakati pawo ndipo anawauza kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+
20 Atanena zimenezi, anawaonetsa manja ake ndi munthiti mwake.+ Choncho ophunzirawo anasangalala ataona Ambuyewo.+
21 Yesu anawauzanso kuti: “Mtendere ukhale nanu.+ Mofanana ndi mmene Atate ananditumira,+ inenso ndikukutumani.”+
22 Atanena zimenezi, anauzira mpweya pa iwo nʼkuwauza kuti: “Landirani mzimu woyera.+
23 Mukakhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu wamukhululukira kale. Koma mukapanda kukhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu sanamukhululukire.”
24 Koma Tomasi,+ amene ankadziwikanso kuti Didimo, mmodzi wa ophunzira 12 aja sanali nawo limodzi pamene Yesu anabwera.
25 Choncho ophunzira enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anawayankha kuti: “Ndikapanda kuona mabala a misomali mʼmanja mwawo ndi kuika chala changa mʼmabala a misomaliwo ndiponso kuika dzanja langa munthiti mwawo,+ ndithu ine sindikhulupirira.”
26 Patapita masiku 8, ophunzira akewo analinso mʼnyumba ndipo Tomasi anali nawo limodzi. Yesu analowa ngakhale kuti zitseko zinali zokhoma ndipo anaimirira pakati pawo nʼkunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+
27 Kenako anauza Tomasi kuti: “Ika chala chako apa ndiponso ona mʼmanja mwangamu. Bweretsa dzanja lako ugwire munthiti mwangamu ndipo usiye kukayikira* koma ukhulupirire.”
28 Tomasi anayankha kuti: “Mbuyanga komanso Mulungu wanga!”
29 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona? Osangalala ndi amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”
30 Kunena zoona, Yesu anachitanso zizindikiro zina zambiri pamaso pa ophunzirawo, zimene sizinalembedwe mumpukutu uno.+
31 Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, komanso chifukwa choti mwakhulupirira, mukhale ndi moyo mʼdzina lake.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”
^ Kapena kuti, “pamanda achikumbutsowo.”
^ Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kukhala wosakhulupirira.”