Mlaliki 3:1-22

  • Chilichonse chili ndi nthawi yake (1-8)

  • Kusangalala ndi moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu (9-15)

    • Anthu ali ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale (11)

  • Mulungu amaweruza anthu onse mwachilungamo (16, 17)

  • Anthu ndi nyama zonse zimafa (18-22)

    • Zonse zimabwerera kufumbi (20)

3  Chilichonse chili ndi nthawi yake,Pali nthawi yochitira chinthu chilichonse padziko lapansi:  2  Pali nthawi yobadwa ndi nthawi yakufa.Nthawi yodzala ndi nthawi yozula chimene chinadzalidwa.  3  Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa.Nthawi yogumula ndi nthawi yomanga.  4  Nthawi yolira ndi nthawi yoseka.Nthawi yolira mofuula ndi nthawi yovina.*  5  Nthawi yotaya miyala ndi nthawi younjika miyala pamodzi.Nthawi yokumbatirana ndi nthawi yopewa kukumbatirana.  6  Nthawi yofunafuna ndi nthawi yovomereza kuti chinthu chatayika.Nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.  7  Nthawi yongʼamba+ ndi nthawi yosoka.Nthawi yokhala chete+ ndi nthawi yolankhula.+  8  Nthawi yachikondi ndi nthawi yachidani.+Nthawi yankhondo ndi nthawi yamtendere. 9  Kodi munthu wogwira ntchito amapeza phindu lanji pa ntchito yonse imene akugwira mwakhama?+ 10  Ndaona ntchito imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azikhala ndi zochita. 11  Chilichonse iye anachipanga chokongola* ndiponso pa nthawi yake.+ Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Komabe anthu sadzadziwa ntchito imene Mulungu woona wagwira kuyambira pachiyambi mpaka pamapeto. 12  Ndazindikira kuti palibe chabwino kuposa kuti iwo asangalale ndiponso kuti azichita zabwino pamene ali ndi moyo,+ 13  komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa nʼkumasangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa cha ntchito yake yonse imene waigwira mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+ 14  Ndazindikira kuti zonse zimene Mulungu woona amapanga zidzakhalapo mpaka kalekale. Palibe choti nʼkuwonjezerapo kapena kuchotsapo. Mulungu woona anazipanga mwanjira imeneyi kuti anthu azimuopa.+ 15  Chilichonse chimene chikuchitika chinachitikapo kale ndipo zimene zidzachitike zinachitikapo kale.+ Koma Mulungu woona amafufuza zinthu zimene anthu akuzifunafuna.* 16  Ine ndaonanso zinthu izi padziko lapansi pano: Pamene panayenera kukhala chilungamo panali zoipa, ndipo pamene panayenera kuchitika zachilungamo panachitika zoipa.+ 17  Choncho mumtima mwanga ndinanena kuti: “Mulungu woona adzaweruza olungama ndi oipa omwe+ chifukwa pali nthawi yoyenera yoti chinthu chilichonse chichitike.” 18  Ndinanenanso mumtima mwanga zokhudza ana a anthu kuti Mulungu woona adzawayesa komanso kuwasonyeza kuti iwo ndi ofanana ndi nyama. 19  Chifukwa anthu ali ndi mapeto ndipo nyamanso zili ndi mapeto. Mapeto a zonsezi ndi ofanana.+ Nyama imafa ndipo munthunso amafa, zonsezi zili ndi mzimu wofanana.+ Choncho munthu saposa nyama, chifukwa zinthu zonse nʼzachabechabe. 20  Zonse zimapita kumalo amodzi.+ Zonse zinachokera kufumbi+ ndipo zonse zimabwerera kufumbi.+ 21  Ndi ndani akudziwa ngati mzimu wa anthu umakwera mʼmwamba ndiponso ngati mzimu wa zinyama umatsika pansi?+ 22  Ndinaona kuti palibe chabwino kuposa kuti munthu asangalale ndi ntchito yake+ chifukwa imeneyo ndi mphoto yake.* Nanga ndi ndani amene angamuchititse kuti aone zimene zidzachitike iye atafa.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “nthawi yodumphadumpha mosangalala.”
Kapena kuti, “chokonzedwa bwino; chadongosolo; choyenerera.”
Mabaibulo ena amati, “zimene zinapita.”
Kapena kuti, “chifukwa limenelo ndi gawo lake.”