Mlaliki 2:1-26
2 Ine ndinadziuza mumtima mwanga kuti: “Ndiyesereko kuchita zinthu zosangalatsa* kuti ndione kuti zili ndi phindu lotani.” Koma ndinaona kuti zimenezinso zinali zachabechabe.
2 Ponena za kuseka ndinanena kuti, “Ndi misala!”
Ndipo ponena za zosangalatsa ndinanena kuti, “Zili ndi phindu lanji?”
3 Ndinayesapo kukhala wokonda kumwa vinyo,+ komabe ndinkaonetsetsa kuti ndikuchita zinthu mwanzeru. Ndinayesanso kuchita zinthu zopusa kuti ndione zinthu zabwino, zimene anthu akuyenera kuchita pa zaka zochepa zimene amakhala ndi moyo padziko lapansi pano.
4 Ndinagwira ntchito zikuluzikulu.+ Ndinamanga nyumba zambirimbiri.+ Ndinalima minda ya mpesa yambirimbiri.+
5 Ndinakonza minda yokongola komanso malo odzalamo maluwa ndi mitengo. Ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso zosiyanasiyana.
6 Ndinapanga madamu a madzi kuti ndizithirira mitengo imene inamera mʼnkhalango yanga.
7 Ndinali ndi antchito aamuna ndi aakazi+ komanso ndinali ndi antchito amene anabadwira mʼnyumba mwanga.* Ndinalinso ndi ziweto zochuluka zedi, ngʼombe ndi nkhosa.+ Zinali zambiri kuposa za onse amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo.
8 Ndinapeza siliva ndi golide wambiri,+ chuma chimene mafumu amakhala nacho* ndiponso chimene chimapezeka mʼzigawo za dziko.+ Ndinali ndi oimba aamuna ndi aakazi. Ndinalinso ndi akazi ambiri, omwe amasangalatsa kwambiri mtima wa amuna.
9 Ndinali ndi zinthu zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu+ ine ndisanakhalepo. Ndipo ndinapitiriza kuchitabe zinthu mwanzeru.
10 Sindinadzimane chilichonse chimene mtima wanga unkalakalaka.*+ Mtima wanga sindinaumane zosangalatsa za mtundu uliwonse. Ndinkasangalala chifukwa cha ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama. Imeneyi inali mphoto yanga* pa ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama.+
11 Koma nditaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira ndiponso ntchito yovuta imene ndinachita khama kuti ndiikwanitse,+ ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe, kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ Padziko lapansi pano panalibe chaphindu chilichonse.+
12 Kenako ndinayamba kuganizaganiza kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani ndiponso kuti uchitsiru nʼchiyani.+ (Kodi munthu amene wabwera pambuyo pa mfumu angachite chiyani? Zimene angachite nʼzimene anthu ena anachita kale.)
13 Ndinaona kuti nzeru nʼzopindulitsa kuposa uchitsiru+ mofanana ndi mmene kuwala kulili kopindulitsa kuposa mdima.
14 Munthu wanzeru maso ake amaona bwino+ koma wopusa amayenda mumdima.+ Komanso ndazindikira kuti zimene zimachitikira onsewa nʼzofanana.+
15 Choncho mumtima mwanga ndinanena kuti: “Zimene zimachitikira opusa inenso zidzandichitikira.”+ Ndiye ndinapindula chiyani chifukwa chokhala wanzeru kwambiri? Choncho mumtima mwanga ndinanena kuti: “Izinso nʼzachabechabe.”
16 Chifukwa munthu wanzeru komanso munthu wopusa,+ onsewa sadzakumbukiridwa mpaka kalekale. Mʼmasiku amene akubwerawa aliyense adzaiwalika. Ndipo kodi wanzeru adzafa bwanji? Adzafa mofanana ndi wopusa.+
17 Choncho ndinayamba kudana ndi moyo+ chifukwa ndinkaona kuti chilichonse chimene chikuchitika padziko lapansi pano chikupangitsa kuti ndizivutika mumtima. Chifukwa zonse zinali zachabechabe,+ zinali ngati kuthamangitsa mphepo.+
18 Ndinayamba kudana ndi zinthu zonse zimene ndinapeza nditagwira ntchito mwakhama padziko lapansi pano,+ chifukwa ndidzayenera kusiyira munthu amene akubwera pambuyo panga.+
19 Ndipo ndi ndani akudziwa ngati angadzakhale wanzeru kapena wopusa?+ Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinapeza nditagwira ntchito mwakhama komanso mwanzeru padziko lapansi pano. Zimenezinso nʼzachabechabe.
20 Choncho ndinayamba kutaya mtima poganizira ntchito yanga yonse yovuta imene ndinagwira mwakhama padziko lapansi pano.
21 Chifukwa munthu akhoza kugwira ntchito mwakhama ndipo angachite zonse mwanzeru, mozindikira komanso mwaluso. Koma amayenerabe kupereka zonse zimene ali nazo kwa munthu amene sanagwire ntchito iliyonse kuti apeze zinthuzo.+ Zimenezinso nʼzachabechabe ndipo nʼzomvetsa chisoni kwambiri.*
22 Kodi munthu amapeza chiyani pa ntchito yonse imene wagwira mwakhama, chifukwa cha zimene amalakalaka mumtima mwake padziko lapansi pano?+
23 Chifukwa masiku onse a moyo wake, ntchito yakeyo imamubweretsera zowawa ndi zokhumudwitsa.+ Ndipo ngakhale usiku mtima wake supuma.+ Izinso nʼzachabechabe.
24 Palibe chabwino kwa munthu kuposa kuti adye, amwe ndi kusangalala chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.+ Ndinazindikira kuti zimenezinso nʼzochokera mʼdzanja la Mulungu woona,+
25 chifukwa ndi ndani amene amamwa ndi kudya bwino kuposa ine?+
26 Munthu amene amasangalatsa Mulungu, Mulunguyo amamʼpatsa nzeru ndi kudziwa zinthu komanso amamuchititsa kuti azisangalala.+ Koma munthu wochimwa amamʼpatsa ntchito yotuta ndi kusonkhanitsa zinthu kuti azipereke kwa munthu amene amasangalatsa Mulungu woona.+ Zimenezinso nʼzachabechabe, zili ngati kuthamangitsa mphepo.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Ndiyesereko kusangalala.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinali ndi ana aamuna a mʼnyumba mwanga.”
^ Kapena kuti, “katundu amene amapezeka ndi mafumu okha.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chimene maso anga anapempha.”
^ Kapena kuti, “Limeneli linali gawo langa.”
^ Kapena kuti, “ndipo ndi tsoka lalikulu.”