Miyambo 3:1-35
3 Mwana wanga, usaiwale zimene ndimakuphunzitsa,*Ndipo mtima wako uzisunga malamulo anga.
2 Ukamachita zimenezi, udzakhala ndi masiku ochulukaKomanso moyo wazaka zambiri ndi mtendere.+
3 Usalole kuti chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika* zichoke mwa iwe.+
Uzimange mʼkhosi mwakoNdi kuzilemba pamtima pako.+
4 Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu+Adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.
5 Uzikhulupirira Yehova+ ndi mtima wako wonse,Ndipo usamadalire* luso lako lomvetsa zinthu.+
6 Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse,+Ndipo iye adzawongola njira zako.+
7 Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+
Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.
8 Zimenezi zidzachiritsa thupi lako*Ndi kutsitsimutsa mafupa ako.
9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+Ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.*+
10 Ukatero nyumba zako zosungiramo zinthu zidzadzaza kwambiri,+Ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano.
11 Mwana wanga, usakane malangizo* a Yehova+Ndipo usanyansidwe ndi kudzudzula kwake,+
12 Chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amamukonda,+Ngati mmene bambo amadzudzulira mwana amene amasangalala naye.+
13 Wosangalala ndi munthu amene amapeza nzeru,+Ndiponso munthu amene amaphunzira zinthu zimene zingamuthandize kukhala wozindikira.
14 Chifukwa kupeza nzeru nʼkwabwino kuposa kupeza siliva,Ndipo kukhala nazo monga phindu nʼkwabwino kuposa kukhala ndi golide.+
15 Nʼzamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,*Palibe chimene umalakalaka chimene chingafanane nazo.
16 Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali.Mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemerero.
17 Kuyenda mʼnjira zake kumasangalatsa,Ndipo kuyenda mʼmisewu yake kumabweretsa mtendere.+
18 Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye,Ndipo anthu amene amazigwiritsitsa adzatchedwa osangalala.+
19 Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru.+
Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.+
20 Chifukwa chakuti iye amadziwa zinthu, anagawa madzi akuyaNdipo kumwamba kwa mitambo kunagwetsa mame.+
21 Mwana wanga, zimenezi* zisachoke pamaso pako.
Uteteze nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.
22 Zidzakupatsa moyoKomanso zidzakhala zokongoletsera mʼkhosi mwako.
23 Ukatero udzayenda panjira yako popanda chokuopseza,Ndipo phazi lako silidzapunthwa.*+
24 Ukagona sudzaopa chilichonse.+Udzagona ndithu, ndipo tulo tako tidzakhala tokoma.+
25 Sudzaopa zoopsa zilizonse zadzidzidzi,+Kapena mphepo yamkuntho imene ikubwera pa oipa.+
26 Chifukwa uzidzadalira kwambiri Yehova,+Ndipo adzateteza phazi lako kuti lisakodwe.+
27 Usalephere kuchitira zabwino anthu amene ukuyenera kuwachitira* zabwinozo,+Ngati ungathe kuwathandiza.*+
28 Mnzako usamuuze kuti, “Pita, ukabwerenso mawa ndipo ndidzakupatsa,”
Ngati ungathe kumupatsa nthawi yomweyo.
29 Usakonze zochitira mnzako zoipa+Pamene iye akuona kuti akukhala nawe mwamtendere.
30 Usakangane ndi munthu popanda chifukwa+Ngati sanakuchitire choipa chilichonse.+
31 Usasirire munthu wachiwawa+Kapena kusankha kuyenda mʼnjira yake iliyonse,
32 Chifukwa Yehova amanyansidwa ndi munthu wachiphamaso,+Koma anthu owongoka mtima amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.+
33 Yehova amatemberera banja la munthu woipa,+Koma iye amadalitsa nyumba ya munthu wolungama.+
34 Onyoza, iye amawanyoza,+Koma ofatsa amawakomera mtima.+
35 Anzeru adzalandira ulemu,Koma opusa amalemekeza zinthu zimene zidzawachititse manyazi.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “usaiwale malamulo anga.”
^ Kapena kuti, “choonadi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “usatsamire.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mchombo wako.”
^ Kapena kuti, “Ndiponso ndi zinthu zabwino kwambiri pa zokolola zako.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Zikuoneka kuti akutanthauza makhalidwe a Mulungu amene atchulidwa mʼmavesi amʼmbuyomu.
^ Kapena kuti, “silidzawomba chilichonse.”
^ Kapena kuti, “Ngati dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.”
^ Kapena kuti, “amene akufunikira.”