Miyambo 16:1-33
16 Munthu amakonza maganizo amumtima mwake,*Koma yankho limene amapereka* limachokera kwa Yehova.+
2 Njira zonse za munthu zimaoneka zabwino* kwa iye,+Koma Yehova amafufuza zolinga zake.+
3 Zochita zako zonse uzisiye mʼmanja mwa Yehova,*+Ndipo mapulani ako adzayenda bwino.
4 Yehova amapangitsa kuti chilichonse chikwaniritse cholinga chake,Ngakhalenso oipa amene adzalangidwe pa tsiku latsoka.+
5 Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.+
Musakayikire mfundo yakuti* munthu wotero sadzalephera kulangidwa.
6 Cholakwa chimaphimbika ndi kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika,+Ndipo chifukwa choopa Yehova, munthu amapewa kuchita zoipa.+
7 Yehova akasangalala ndi njira za munthu,Amachititsa ngakhale adani a munthuyo kukhala naye pamtendere.+
8 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa koma uli wachilungamo+Kusiyana nʼkupeza zinthu zambiri mopanda chilungamo.+
9 Munthu angakhale ndi pulani ya zimene akufuna kuchita pa moyo wake,Koma Yehova ndi amene amatsogolera mapazi ake.+
10 Chigamulo chilichonse chimene mfumu ikupereka chizikhala chogwirizana ndi malangizo ochokera kwa Mulungu.+Mfumuyo isamakhotetse chilungamo.+
11 Miyezo komanso masikelo achilungamo ndi ochokera kwa Yehova.Miyala yonse yoyezera imene ili mʼthumba anaipanga ndi iyeyo.+
12 Mafumu abwino amadana ndi kuchita zinthu zoipa,+Chifukwa mpando wawo wachifumu umakhazikika akamalamulira mwachilungamo.+
13 Mawu achilungamo amasangalatsa mafumu.
Iwo amakonda munthu amene amalankhula moona mtima.+
14 Mkwiyo wa mfumu uli ngati mthenga wa imfa,+Koma munthu wanzeru amauziziritsa.*+
15 Mfumu ikamukomera munthu mtima, munthuyo amakhala ndi moyo wabwino.Kukoma mtima kwake kuli ngati mtambo wa mvula mʼnyengo ya chilimwe.+
16 Kupeza nzeru nʼkwabwino kwambiri kuposa kupeza golide.+
Ndipo ndi bwino kusankha kumvetsa zinthu kuposa siliva.+
17 Anthu owongoka mtima amapewa kuchita zinthu zoipa.
Aliyense amene amateteza njira yake, amasunga moyo wake.+
18 Kunyada kumachititsa kuti munthu awonongeke,Ndipo mtima wodzikuza umachititsa kuti munthu apunthwe.+
19 Kuli bwino kukhala wodzichepetsa pakati pa anthu ofatsa,+Kusiyana nʼkugawana katundu amene anthu odzikuza alanda.
20 Munthu wosonyeza kuzindikira pochita zinthu, zidzamuyendera bwino,Ndipo wosangalala ndi munthu amene amadalira Yehova.
21 Munthu wa mtima wanzeru adzatchedwa wozindikira,+Ndipo amene amalankhula mokoma mtima* amakopa ena ndi mawu akewo.+
22 Kuzindikira kuli ngati kasupe wa moyo kwa ozindikirawo,Koma zitsiru zimalangidwa ndi kupusa kwawo komwe.
23 Munthu wanzeru amasankha mawu mwanzeru akamalankhula,+Ndipo mawu ake amakopa anthu ena.
24 Mawu okoma ali ngati chisa cha uchi.Amakhala okoma kwa munthu ndipo amachiritsa mafupa.+
25 Pali njira imene imaoneka ngati yabwino kwa munthu,Koma pamapeto pake imabweretsa imfa.+
26 Munthu amagwira ntchito mwakhama kuti apeze chakudya.Chifukwa njala imamuchititsa* kuti apitirize kugwira ntchito.+
27 Munthu wopanda pake amafukula zinthu zoipa,+Ndipo zimene amalankhula zili ngati moto umene ukuyaka.+
28 Munthu woyambitsa mavuto* amayambanitsa anthu,+Ndipo wonenera anzake zoipa amalekanitsa mabwenzi apamtima.+
29 Munthu wachiwawa amakopa mnzake kuti achite zoipa,Ndipo amamuchititsa kuti ayende mʼnjira yolakwika.
30 Akamakonza ziwembu, amatsinzinira maso ake.
Ndipo akamachita zinthu zosayenera amalumira milomo yake.
31 Imvi ndi chisoti chachifumu cha ulemerero+Zikapezeka ndi munthu amene akuyenda mʼnjira yachilungamo.+
32 Munthu wosakwiya msanga+ ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu,Ndipo munthu amene amalamulira mkwiyo wake amaposa munthu amene wagonjetsa mzinda.+
33 Maere amaponyedwa pachovala,+Koma zonse zimene maerewo asonyeza zimachokera kwa Yehova.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “yankho lolondola.” Mʼchilankhulo choyambirira, “yankho la lilime.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Munthu ndi amene amaika maganizo amumtima mwake mwadongosolo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “zoyera.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Pereka ntchito zako kwa Yehova.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngakhale dzanja ligwirane ndi dzanja linzake.”
^ Kapena kuti, “amaupewa.”
^ Kapena kuti, “mawu osangalatsa.” Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi milomo yotsekemera.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwa pamamuchititsa.”
^ Kapena kuti, “wokonza ziwembu.”