Salimo 46:1-11
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora.+ Mogwirizana ndi kaimbidwe ka Alamoti.* Nyimbo.
46 Mulungu ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu,+Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.+
2 Nʼchifukwa chake sitidzaopa, ngakhale dziko lapansi litasintha,Ndiponso ngakhale mapiri atagwera mʼnyanja yakuya nʼkumira,+
3 Ngakhale madzi amʼnyanjayo atawinduka nʼkuchita thovu,+Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka chifukwa cha kuwinduka kwa nyanjayo. (Selah)
4 Pali mtsinje umene nthambi zake zimachititsa kuti anthu amumzinda wa Mulungu asangalale,+Chihema chachikulu chopatulika cha Wamʼmwambamwamba.
5 Mulungu ali mumzindawo+ ndipo sungagonjetsedwe.
Mulungu adzauthandiza mʼbandakucha.+
6 Mitundu ya anthu inachita phokoso, maufumu anagonjetsedwa.Iye analankhula mokweza mawu ndipo dziko lapansi linasungunuka.+
7 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ali ndi ife.+Mulungu wa Yakobo ndi malo athu othawirako otetezeka.* (Selah)
8 Bwerani mudzaone ntchito za Yehova,Mmene wachitira zinthu zodabwitsa padziko lapansi.
9 Akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi.+
Wathyola uta ndi kupindapinda mkondo.Ndipo wawotcha pamoto magaleta ankhondo.*
10 “Gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu.
Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu,+Ndidzakwezedwa padziko lapansi.”+
11 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ali ndi ife.+Mulungu wa Yakobo ndi malo athu othawirako otetezeka.+ (Selah)
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
^ Mabaibulo ena amati, “zishango.”