Machitidwe a Atumwi 3:1-26
3 Tsopano Petulo ndi Yohane ankapita kukalowa mʼkachisi pa nthawi yokapemphera, 3 koloko masana.*
2 Ndiyeno panali mwamuna wina amene anabadwa ali wolumala. Tsiku lililonse ankamunyamula nʼkumukhazika pafupi ndi khomo la kachisi lotchedwa Geti Lokongola, kuti azipempha mphatso zachifundo kwa anthu olowa mʼkachisimo.
3 Munthuyu ataona Petulo ndi Yohane akukalowa mʼkachisimo, anayamba kupempha kuti amupatse mphatso zachifundo.
4 Koma Petulo, pamodzi ndi Yohane, anamuyangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Tiyangʼane.”
5 Iye anawayangʼanitsitsa, akuyembekeza kuti amupatsa kanthu.
6 Koma Petulo anati: “Siliva ndi golide ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda!”+
7 Atatero anamugwira dzanja lamanja nʼkumuimiritsa.+ Nthawi yomweyo mapazi ndi miyendo* yake zinalimba.+
8 Zitatero anadumpha nʼkuimirira+ ndipo anayamba kuyenda. Iye analowa nawo limodzi mʼkachisimo, akuyenda, kudumphadumpha komanso kutamanda Mulungu.
9 Anthu onse anamuona akuyenda ndi kutamanda Mulungu.
10 Iwo anamuzindikira kuti ndi munthu amene ankakhala pa Geti Lokongola la kachisi+ nʼkumapempha mphatso zachifundo. Ndipo anthuwo anadabwa kwambiri ndi zimene zinamuchitikirazo.
11 Munthu uja ankangoyendabe ndi Petulo ndi Yohane osawasiya, ndipo gulu lonse la anthu linathamangira kwa iwo pamalo otchedwa Khonde la Zipilala la Solomo,+ likudabwa kwambiri.
12 Petulo ataona zimenezi, anauza anthuwo kuti: “Aisiraeli inu, nʼchifukwa chiyani mukudabwa nazo zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukutiyangʼanitsitsa ngati kuti tamuyendetsa ndi mphamvu zathu kapena chifukwa cha kudzipereka kwathu kwa Mulungu?
13 Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo,+ Mulungu wa makolo athu, ndi amene walemekeza Mtumiki wake+ Yesu,+ amene inu munamupereka+ ndiponso kumukana pamaso pa Pilato, ngakhale kuti Pilatoyo ankafuna kumumasula.
14 Inde, inu munakana woyera ndi wolungamayo, ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wopha anthu.+
15 Munapha Mtumiki Wamkulu wa moyo,+ koma Mulungu anamuukitsa ndipo ife ndife mboni za nkhani imeneyi.+
16 Choncho mʼdzina lake komanso chifukwa choti timakhulupirira dzina lakelo, munthu amene mukumuona ndiponso kumudziwayu wachira. Chikhulupiriro chimene ife tili nacho chifukwa cha iye chachititsa kuti achiriretu ngati mmene nonsenu mukuonera.
17 Abale anga, ndikudziwa kuti munachita zinthu mosazindikira,+ ngati mmenenso olamulira anu anachitira.+
18 Koma pamenepa Mulungu wakwaniritsa zimene analengezeratu kudzera mwa aneneri onse, kuti Khristu wake adzavutika.+
19 Choncho lapani+ ndi kutembenuka+ kuti machimo anu afafanizidwe,+ ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwere kuchokera kwa Yehova.*
20 Komanso kuti atumize Yesu, amene ndi Khristu wosankhidwa chifukwa cha inu.
21 Ameneyu kumwamba kuyenera kumusunga mpaka nthawi yobwezeretsa zinthu zonse, imene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri ake oyera akale.
22 Ndipotu Mose ananena kuti, ‘Yehova* Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine kuchokera pakati pa abale anu.+ Mudzamumvere pa zinthu zonse zimene adzakuuzeni.+
23 Munthu aliyense amene sadzamvera Mneneriyo, Mulungu adzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu.’+
24 Ndipo aneneri onse, kuyambira pa Samueli mpaka aneneri onse amene anabwera mʼmbuyo mwake, onse amene analosera, ananena mosapita mʼmbali za masiku amenewa.+
25 Inu ndinu ana a aneneri ndi a pangano limene Mulungu anapangana ndi makolo anu akale.+ Iye anauza Abulahamu kuti: ‘Kudzera mwa mbadwa* yako mabanja onse apadziko lapansi adzadalitsidwa.’+
26 Mulungu atasankha Mtumiki wake, choyamba+ anamutumiza kwa inu, kuti adzakudalitseni pobweza aliyense wa inu kuti musiye ntchito zanu zoipa.”
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.
^ Kutanthauza timafupa tomwe timalumikiza phazi ndi mwendo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera pankhope ya Yehova.” Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”