Machitidwe a Atumwi 14:1-28
14 Paulo ndi Baranaba ali ku Ikoniyo, analowa mʼsunagoge wa Ayuda ndipo analankhula bwino kwambiri moti Ayuda ambiri limodzi ndi Agiriki anakhala okhulupirira.
2 Koma Ayuda amene sanakhulupirire, anauza zoipa anthu a mitundu ina nʼkuwasokoneza maganizo kuti atsutsane ndi abalewo.+
3 Choncho kwa nthawi yaitali, ankalankhula molimba mtima chifukwa cha mphamvu ya Yehova.* Iye anatsimikizira mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu, polola kuti ophunzirawo azichita zizindikiro ndi zodabwitsa.+
4 Koma gulu la anthu mumzindawo linagawanika. Ena anali kumbali ya Ayuda, ena kumbali ya atumwi.
5 Ndiyeno anthu a mitundu ina komanso Ayuda pamodzi ndi olamulira awo, anakonza chiwembu kuti achitire chipongwe atumwiwo nʼkuwaponya miyala.+
6 Koma iwo atadziwitsidwa zimenezi, anathawira mʼmizinda ya Lukaoniya, Lusitara, Debe, ndi mʼmadera ozungulira.+
7 Kumeneko anapitiriza kulalikira uthenga wabwino.
8 Ku Lusitara, kunali munthu wina wolumala miyendo ndipo anali atakhala pansi. Iyeyu anabadwa wolumala ndipo anali asanayendepo.
9 Munthu ameneyu ankamvetsera pamene Paulo ankalankhula. Ndiyeno Paulo atamuyangʼanitsitsa anaona kuti ali ndi chikhulupiriro choti angachiritsidwe.+
10 Choncho Paulo analankhula mokweza mawu kuti: “Imirira!” Atatero, wolumalayo anadumpha nʼkuyamba kuyenda.+
11 Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazo, linafuula mʼchilankhulo cha Chilukaoniya kuti: “Milungu yakhala ngati anthu ndipo yatsikira kwa ife!”+
12 Choncho Baranaba anayamba kumutchula kuti Zeu, koma Paulo ankamutchula kuti Heme, chifukwa ndi amene ankatsogolera polankhula.
13 Ndiyeno wansembe wa Zeu, amene kachisi wake anali pafupi ndi polowera mumzindawo, anabweretsa ngʼombe zamphongo ndi nkhata zamaluwa pamageti. Iye ankafuna kupereka nsembe pamodzi ndi gulu la anthulo.
14 Koma atumwiwo, Baranaba ndi Paulo, atamva zimenezi anangʼamba malaya awo akunja nʼkuthamanga kukalowa mʼgulu la anthu lija akufuula kuti:
15 “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.+ Tikulengeza uthenga wabwino kwa inu kuti musiye zinthu zachabechabezi nʼkuyamba kulambira Mulungu wamoyo, amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.+
16 Mʼmibadwo yamʼmbuyomu iye analola anthu a mitundu yonse kuti aziyenda mʼnjira zawo.+
17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni+ wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri.+ Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chisangalalo.”+
18 Ngakhale kuti atumwiwo ananena zimenezi, anavutikabe kuletsa gulu la anthulo kupereka nsembe kwa iwo.
19 Ndiyeno Ayuda amene anabwera kuchokera ku Antiokeya ndi ku Ikoniyo anakopa anthuwo.+ Choncho anaponya Paulo miyala nʼkumukokera kunja kwa mzindawo poganiza kuti wafa.+
20 Koma pamene ophunzira anamuzungulira, anadzuka nʼkukalowa mumzinda. Tsiku lotsatira iye pamodzi ndi Baranaba anachoka nʼkupita ku Debe.+
21 Atalengeza uthenga wabwino mumzindawu nʼkuphunzitsa anthu ambiri ndithu kuti akhale ophunzira, anabwerera ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya.
22 Mʼmalo onsewa ankalimbitsa ophunzira+ komanso kuwathandiza kuti apitirize kukhala ndi chikhulupiriro. Ankawauza kuti: “Tiyenera kukumana ndi mavuto ambiri kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.”+
23 Anasankhanso akulu mumpingo uliwonse,+ ndipo atapemphera komanso kusala kudya,+ anawapereka kwa Yehova* yemwe anamukhulupirira.
24 Kenako anadutsa ku Pisidiya nʼkupita ku Pamfuliya.+
25 Atamaliza kulalikira mawu a Mulungu ku Pega, anapita ku Ataliya.
26 Pochoka kumeneko anayenda ulendo wapamadzi kubwerera ku Antiokeya. Kumeneku nʼkumene mʼmbuyomo abale anawasankha kuti Mulungu awasonyeze kukoma mtima kwakukulu nʼcholinga choti agwire ntchito, yomwe tsopano pa nthawiyi anali ataimaliza.+
27 Atafika kumeneko anasonkhanitsa anthu amumpingo ndipo anawafotokozera zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo. Anawafotokozeranso kuti Mulungu anatsegulanso khomo kuti anthu a mitundu ina akhale okhulupirira.+
28 Choncho anakhala ndi ophunzirawo kwa kanthawi ndithu.