1 Samueli 1:1-28

  • Elikana ndi akazi ake (1-8)

  • Hana anapemphera kuti akhale ndi mwana (9-18)

  • Samueli anabadwa nʼkuperekedwa kwa Yehova (19-28)

1  Panali mwamuna wina wa ku Ramatayimu-zofimu,*+ kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Elikana.+ Iye anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufi, ndipo anali wa fuko la Efuraimu. 2  Elikana anali ndi akazi awiri. Mkazi wina anali Hana ndipo wina anali Penina. Penina anali ndi ana koma Hana analibe ana. 3  Chaka chilichonse mwamuna ameneyu ankachoka mumzinda wawo nʼkupita ku Silo, kukalambira* Yehova wa magulu ankhondo akumwamba komanso kukapereka nsembe zake.+ Kumeneko nʼkumene ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinihasi,+ ankatumikira monga ansembe a Yehova.+ 4  Tsiku lina pamene Elikana ankapereka nsembe, anatenga magawo a nsembeyo nʼkupereka kwa mkazi wake Penina komanso ana ake onse aamuna ndi aakazi.+ 5  Koma Hana anamʼpatsa gawo lapadera chifukwa ndi amene ankamukonda, komabe Yehova sanamupatse ana.* 6  Komanso mkazi mnzake wa Hana ankamusautsa kwambiri nʼcholinga choti amukhumudwitse chifukwa Yehova sanamupatse ana. 7  Ankachita zimenezi chaka chilichonse Hana akapita kunyumba ya Yehova.+ Penina ankamuzunza kwambiri moti Hana ankalira ndipo sankadya. 8  Ndiyeno Elikana mwamuna wake anati: “Hana, nʼchifukwa chiyani ukulira, ndipo nʼchifukwa chiyani sukudya? Komanso nʼchifukwa chiyani wakhumudwa chonchi? Kodi sindikuposa ana aamuna 10 kwa iwe?” 9  Atamaliza kudya ndi kumwa ku Silo, Hana anaimirira. Apa nʼkuti Eli wansembe atakhala pampando, pakhomo la kachisi*+ wa Yehova. 10  Hana anali wokhumudwa kwambiri ndipo anayamba kupemphera kwa Yehova+ uku akulira kwambiri. 11  Iye analonjeza kuti: “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, mukaona kuvutika kwa ine kapolo wanu nʼkundikumbukira ndiponso mukapanda kundiiwala ine kapolo wanu nʼkundipatsa mwana wamwamuna,+ ndidzamʼpereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake ndipo lezala silidzadutsa mʼmutu mwake.”+ 12  Pamene ankapemphera kwa Yehova kwa nthawi yaitali chonchi, Eli ankayangʼanitsitsa pakamwa pake. 13  Hana ankalankhula chamumtima. Milomo yake inkanjenjemera koma sankatulutsa mawu. Eli ataona zimenezi anaganiza kuti waledzera. 14  Ndipo anamuuza kuti: “Kodi ukhala woledzera mpaka liti? Siya kumwa vinyo wakoyo.” 15  Koma Hana anayankha kuti: “Ayi mbuyanga! Munthune ndili ndi nkhawa kwambiri. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, koma ndikufotokozera Yehova nkhawa zanga zonse.+ 16  Musaone ngati ine kapolo wanu ndine mkazi wopanda pake, popeza ndakhala ndikulankhula mpaka pano chifukwa cha kukhumudwa kwambiri ndiponso nkhawa.” 17  Zitatero Eli anamuyankha kuti: “Pita mumtendere, ndipo Mulungu wa Isiraeli akupatse zimene wamupempha.”+ 18  Hana anayankha kuti: “Pitirizani kundikomera mtima ine kapolo wanu.” Ndiyeno anachoka nʼkupita kukadya ndipo nkhope yake sinkaonekanso ya nkhawa. 19  Kenako anadzuka mʼmawa ndipo atalambira Yehova anabwerera kunyumba kwawo ku Rama.+ Ndiyeno Elikana anagona ndi mkazi wake Hana ndipo Yehova anamukumbukira.+ 20  Chaka chisanathe, Hana anatenga pakati nʼkubereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina+ lakuti Samueli* chifukwa anati, “ndinamupempha kwa Yehova.” 21  Patapita nthawi, Elikana anapita ndi banja lake lonse kukapereka kwa Yehova nsembe yapachaka+ ndi nsembe yake yalonjezo. 22  Koma Hana sanapite nawo,+ chifukwa anali atauza mwamuna wake kuti: “Mwanayu akadzangosiya kuyamwa, ndidzapita naye. Kenako adzaonekera pamaso pa Yehova ndipo azikakhala komweko.”+ 23  Elikana anamuuza kuti: “Chita zimene ukuona kuti nʼzabwino kwa iweyo. Ukhoza kukhala mpaka mwanayo atasiya kuyamwa. Yehova akwaniritse zimene iwe wanena.” Choncho Hana anakhalabe pakhomo ndipo anapitiriza kulera mwana wakeyo mpaka atasiya kuyamwa. 24  Mwanayo atangosiya kuyamwa, Hana anapita naye ku Silo atatenga ngʼombe yaingʼono yamphongo yazaka zitatu, ufa wokwana muyezo umodzi wa efa* ndi mtsuko wa vinyo.+ Iye analowa mʼnyumba ya Yehova ku Silo+ limodzi ndi mwanayo. 25  Kenako iwo anapha ngʼombe yaingʼono yamphongoyo ndipo anapita ndi mwanayo kwa Eli. 26  Ndiyeno ananena kuti: “Pepani mbuyanga muli apa.* Ine ndine mayi uja amene ndinabwera nʼkuima pamalo ano, nʼkumapemphera kwa Yehova.+ 27  Ndinkapempha kuti andipatse mwana wamwamunayu ndipo Yehova wandipatsa zimene ndinapempha.+ 28  Ndipo ine ndikumupereka kwa Yehova. Ndikumupereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.” Kenako iye* anagwada nʼkulambira Yehova.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wa ku Rama, wa mʼbanja la Zufi.”
Kapena kuti, “kukawerama pamaso pa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anali atatseka mimba yake.”
Chimenechi chinali chihema.
Kutanthauza “Dzina la Mulungu.”
Pafupifupi malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “Pali moyo wanu mbuyanga.”
Ayenera kuti ndi Elikana.